Lamentations 4 (BOGWICC)

1 Haa! Golide wathimbirira,golide wosalala wasinthikiratu!Amwazamwaza miyala yokongola ya kumalo opatulikapamphambano ponse pa mzinda. 2 Haa! Ana a Ziyoni amtengowapataliamene kale anali ngati golide,tsopano ali ngati miphika ya dothi,ntchito ya owumba mbiya! 3 Ngakhale nkhandwe zimapereka berekuyamwitsa ana ake,koma anthu anga asanduka ankhanzangati nthiwatiwa mʼchipululu. 4 Lilime la mwana lakangamira kukhosichifukwa cha ludzu,ana akupempha chakudya,koma palibe amene akuwapatsa. 5 Iwo amene kale ankadya zononaakupemphetsa mʼmisewu ya mu mzinda.Iwo amene kale ankavala zokongolatsopano akugona pa phulusa. 6 Kuyipa kwa anthu anga kunali kwakukulukuposa anthu a ku Sodomu,amene anawonongedwa mʼkamphindi kochepapopanda owathandiza. 7 Akalonga ake anali owala koposa chisanu chowundanandi oyera kuposa mkaka.Matupi awo anali ofiira kuposa miyala ya rubi,maonekedwe awo ngati miyala ya safiro. 8 Koma tsopano maonekedwe awo ndi akuda kuposa mwaye;palibe angawazindikire mʼmisewu ya mu mzinda.Khungu lawo lachita makwinyamakwinya pa mafupa awo;lawuma gwaa ngati nkhuni. 9 Amene anaphedwa ndi lupanga aliko bwino kuposaamene anafa ndi njala;chifukwa chosowa chakudya cha mʼmundaiwowa ankafowoka ndi njala mpaka kufa. 10 Amayi achifundo afikapophika ana awo enieni,ndiwo anali chakudya chawo pamene anthuanga anali kuwonongeka. 11 Yehova wakwaniritsa ukali wake;wagwetsa pansi mkwiyo wake woopsa.Ndipo wayatsa moto mʼZiyonikuti uwononge maziko ake. 12 Mafumu a pa dziko lapansi sanakhulupirire,kapena wina aliyense wokhala pa dziko lonse,kuti adani kapena ankhondo akhoza kulowapa zipata za Yerusalemu. 13 Koma izi zinachitika chifukwa cha kuchimwa kwa aneneri akendi mphulupulu za ansembe ake,amene ankapha anthu osalakwa pakati pawo. 14 Tsopano akungoyendayenda mʼmisewu ya mu mzindangati anthu osaona.Iwo ndi odetsedwa kwambiri ndi magazipalibe yemwe angayerekeze nʼkukhudza komwe chovala chawo. 15 Anthu akuwafuwulira kuti, “Chokani! Inu anthu odetsedwa!”“Chokani! Chokani! Musatikhudze ife!”Akamathawa ndi kumangoyendayenda,pakati pa anthu a mitundu yonse amati,“Asakhalenso ndi ife.” 16 Yehova mwini wake wawabalalitsa;Iye sakuwalabadiranso.Ansembe sakulandira ulemu,akuluakulu sakuwachitira chifundo. 17 Ndiponso maso athu atopa nʼkuyangʼana,chithandizo chosabwera nʼkomwe,kuchokera pa nsanja zathu tinadikirira mtunduwa anthu umene sukanatipulumutsa. 18 Anthu ankalondola mapazi athu,choncho sitikanayenda mʼmisewu yathu mu mzinda.Chimaliziro chathu chinali pafupi, masiku athu anali owerengeka,chifukwa chimaliziro chathu chinali chitafika. 19 Otilondola akuthamanga kwambirikuposa ziwombankhanga mu mlengalenga;anatithamangitsa mpaka ku mapirindi kutibisalira mʼchipululu. 20 Wodzozedwa wa Yehova, mpweya wathu wotipatsa moyo,anakodwa mʼmisampha yawo.Tinaganiza kuti tidzakhala pansi pa mthunzi wakepakati pa mitundu ya anthu. 21 Kondwera ndi kusangalala, mwana wamkazi wa Edomu.Iwe amene umakhala mʼdziko la Uzi.Koma iwenso chikho chidzakupeza;udzaledzera mpaka kukhala maliseche. 22 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, chilango chako chidzatha;Iye sadzatalikitsa nthawi yako ya ukapolo.Koma Yehova adzalanga machimo ako, iwe mwana wamkazi wa Edomu,ndi kuyika poyera mphulupulu zako.

In Other Versions

Lamentations 4 in the ANGEFD

Lamentations 4 in the ANTPNG2D

Lamentations 4 in the AS21

Lamentations 4 in the BAGH

Lamentations 4 in the BBPNG

Lamentations 4 in the BBT1E

Lamentations 4 in the BDS

Lamentations 4 in the BEV

Lamentations 4 in the BHAD

Lamentations 4 in the BIB

Lamentations 4 in the BLPT

Lamentations 4 in the BNT

Lamentations 4 in the BNTABOOT

Lamentations 4 in the BNTLV

Lamentations 4 in the BOATCB

Lamentations 4 in the BOATCB2

Lamentations 4 in the BOBCV

Lamentations 4 in the BOCNT

Lamentations 4 in the BOECS

Lamentations 4 in the BOHCB

Lamentations 4 in the BOHCV

Lamentations 4 in the BOHLNT

Lamentations 4 in the BOHNTLTAL

Lamentations 4 in the BOICB

Lamentations 4 in the BOILNTAP

Lamentations 4 in the BOITCV

Lamentations 4 in the BOKCV

Lamentations 4 in the BOKCV2

Lamentations 4 in the BOKHWOG

Lamentations 4 in the BOKSSV

Lamentations 4 in the BOLCB

Lamentations 4 in the BOLCB2

Lamentations 4 in the BOMCV

Lamentations 4 in the BONAV

Lamentations 4 in the BONCB

Lamentations 4 in the BONLT

Lamentations 4 in the BONUT2

Lamentations 4 in the BOPLNT

Lamentations 4 in the BOSCB

Lamentations 4 in the BOSNC

Lamentations 4 in the BOTLNT

Lamentations 4 in the BOVCB

Lamentations 4 in the BOYCB

Lamentations 4 in the BPBB

Lamentations 4 in the BPH

Lamentations 4 in the BSB

Lamentations 4 in the CCB

Lamentations 4 in the CUV

Lamentations 4 in the CUVS

Lamentations 4 in the DBT

Lamentations 4 in the DGDNT

Lamentations 4 in the DHNT

Lamentations 4 in the DNT

Lamentations 4 in the ELBE

Lamentations 4 in the EMTV

Lamentations 4 in the ESV

Lamentations 4 in the FBV

Lamentations 4 in the FEB

Lamentations 4 in the GGMNT

Lamentations 4 in the GNT

Lamentations 4 in the HARY

Lamentations 4 in the HNT

Lamentations 4 in the IRVA

Lamentations 4 in the IRVB

Lamentations 4 in the IRVG

Lamentations 4 in the IRVH

Lamentations 4 in the IRVK

Lamentations 4 in the IRVM

Lamentations 4 in the IRVM2

Lamentations 4 in the IRVO

Lamentations 4 in the IRVP

Lamentations 4 in the IRVT

Lamentations 4 in the IRVT2

Lamentations 4 in the IRVU

Lamentations 4 in the ISVN

Lamentations 4 in the JSNT

Lamentations 4 in the KAPI

Lamentations 4 in the KBT1ETNIK

Lamentations 4 in the KBV

Lamentations 4 in the KJV

Lamentations 4 in the KNFD

Lamentations 4 in the LBA

Lamentations 4 in the LBLA

Lamentations 4 in the LNT

Lamentations 4 in the LSV

Lamentations 4 in the MAAL

Lamentations 4 in the MBV

Lamentations 4 in the MBV2

Lamentations 4 in the MHNT

Lamentations 4 in the MKNFD

Lamentations 4 in the MNG

Lamentations 4 in the MNT

Lamentations 4 in the MNT2

Lamentations 4 in the MRS1T

Lamentations 4 in the NAA

Lamentations 4 in the NASB

Lamentations 4 in the NBLA

Lamentations 4 in the NBS

Lamentations 4 in the NBVTP

Lamentations 4 in the NET2

Lamentations 4 in the NIV11

Lamentations 4 in the NNT

Lamentations 4 in the NNT2

Lamentations 4 in the NNT3

Lamentations 4 in the PDDPT

Lamentations 4 in the PFNT

Lamentations 4 in the RMNT

Lamentations 4 in the SBIAS

Lamentations 4 in the SBIBS

Lamentations 4 in the SBIBS2

Lamentations 4 in the SBICS

Lamentations 4 in the SBIDS

Lamentations 4 in the SBIGS

Lamentations 4 in the SBIHS

Lamentations 4 in the SBIIS

Lamentations 4 in the SBIIS2

Lamentations 4 in the SBIIS3

Lamentations 4 in the SBIKS

Lamentations 4 in the SBIKS2

Lamentations 4 in the SBIMS

Lamentations 4 in the SBIOS

Lamentations 4 in the SBIPS

Lamentations 4 in the SBISS

Lamentations 4 in the SBITS

Lamentations 4 in the SBITS2

Lamentations 4 in the SBITS3

Lamentations 4 in the SBITS4

Lamentations 4 in the SBIUS

Lamentations 4 in the SBIVS

Lamentations 4 in the SBT

Lamentations 4 in the SBT1E

Lamentations 4 in the SCHL

Lamentations 4 in the SNT

Lamentations 4 in the SUSU

Lamentations 4 in the SUSU2

Lamentations 4 in the SYNO

Lamentations 4 in the TBIAOTANT

Lamentations 4 in the TBT1E

Lamentations 4 in the TBT1E2

Lamentations 4 in the TFTIP

Lamentations 4 in the TFTU

Lamentations 4 in the TGNTATF3T

Lamentations 4 in the THAI

Lamentations 4 in the TNFD

Lamentations 4 in the TNT

Lamentations 4 in the TNTIK

Lamentations 4 in the TNTIL

Lamentations 4 in the TNTIN

Lamentations 4 in the TNTIP

Lamentations 4 in the TNTIZ

Lamentations 4 in the TOMA

Lamentations 4 in the TTENT

Lamentations 4 in the UBG

Lamentations 4 in the UGV

Lamentations 4 in the UGV2

Lamentations 4 in the UGV3

Lamentations 4 in the VBL

Lamentations 4 in the VDCC

Lamentations 4 in the YALU

Lamentations 4 in the YAPE

Lamentations 4 in the YBVTP

Lamentations 4 in the ZBP