Mark 8 (BOGWICC)

1 Mʼmasiku amenewo gulu lina lalikulu la anthu linasonkhana. Popeza iwo analibe chakudya, Yesu anayitana ophunzira ake nati kwa iwo, 2 “Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala ali ndi Ine masiku atatuwa ndipo alibe chakudya. 3 Ngati nditawawuza kuti apite kwawo ali ndi njala, iwo adzakomoka mʼnjira chifukwa ena a iwo achokera kutali.” 4 Ophunzira ake anayankha nati, “Kodi ndi kuti kuthengo kuno kumene munthu angapeze buledi okwanira kuwadyetsa?” 5 Yesu anafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?”Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.” 6 Iye anawuza gulu la anthu kuti likhale pansi. Atatenga malofu a buledi asanu ndi awiri, anayamika, nawanyema ndipo anapatsa ophunzira ake kuti agawire anthu, ndipo iwo anatero. 7 Analinso ndi tinsomba tochepa; Iye anayamikanso chifukwa cha nsombazo. Ndipo anawuza ophunzira kuti awagawire. 8 Anthu anadya ndipo anakhuta. Atamaliza, ophunzira anatola buledi ndi nsomba zotsalira ndi kudzaza madengu asanu ndi awiri. 9 Panali amuna pafupifupi 4,000. Ndipo atawawuza kuti apite kwawo, 10 analowa mʼbwato pamodzi ndi ophunzira ake napita ku dera la Dalamanuta. 11 Afarisi anabwera nayamba kumufunsa Yesu. Pomuyesa Iye, anamufunsa za chizindikiro chochokera kumwamba. 12 Ndipo anatsitsa moyo nati, “Nʼchifukwa chiyani mʼbado uno ukufuna chizindikiro chodabwitsa? Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe chizindikiro chidzapatsidwa kwa iwo.” 13 Ndipo anawasiya, nalowanso mʼbwato ndi kuwolokera tsidya lina. 14 Ophunzira anayiwala kutenga buledi, kupatula buledi mmodzi yekha amene anali naye mʼbwato. 15 Yesu anawachenjeza kuti, “Samalani ndipo onetsetsani yisiti wa Afarisi ndi wa Herode.” 16 Iwo anakambirana wina ndi mnzake ndipo anati, “Ndi chifukwa choti tilibe buledi.” 17 Yesu atadziwa zokambirana zawo anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukukambirana kuti mulibe buledi? Kodi inu simukuonabe kapena kuzindikira? Kodi mitima yanu ndi yowumitsidwa? 18 Kodi muli ndi maso ndipo simukuona, ndi makutu ndipo mukulephera kumva? Kodi simukukumbukira? 19 Pamene ndinagawa malofu asanu a buledi kwa anthu 5,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”Iwo anayankha kuti, “Khumi ndi awiri.” 20 “Ndipo pamene ndinagawa malofu asanu ndi awiri a buledi, kwa anthu 4,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.” 21 Iye anawafunsa kuti, “Kodi simumvetsetsabe?” 22 Iwo anafika ku Betisaida, ndipo anthu ena anabweretsa munthu wosaona ndipo anamupempha Yesu kuti amukhudze. 23 Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo napita naye kunja kwa mudzi. Atalavulira mʼmaso a munthuyo ndi kumusanjika manja, Yesu anafunsa kuti, “Kodi ukuona kalikonse?” 24 Iye anakweza maso nati, “Ndikuona anthu; akuoneka ngati mitengo imene ikuyendayenda.” 25 Kenakanso Yesu anayika manja ake mʼmaso a munthuyo. Ndipo maso ake anatsekuka, naonanso, ndipo anaona zonse bwinobwino. 26 Yesu anamuwuza kuti apite kwawo nati, “Usapite mʼmudzimo.” 27 Yesu ndi ophunzira ake anapita ku midzi yozungulira Kaisareya wa Filipo. Ali panjira, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati ndine yani?” 28 Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneri.” 29 Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu, mumati ndine yani?”Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu.” 30 Yesu anawachenjeza kuti asawuze wina aliyense za Iye. 31 Iye anayamba kuwaphunzitsa kuti, “Mwana wa Munthu ayenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe, ndi aphunzitsi a malamulo, ndi kuti ayenera kuphedwa ndipo patatha masiku atatu adzaukanso.” 32 Izi anaziyankhula momveka bwino, ndipo Petro anamutengera pambali ndipo anayamba kumudzudzula. 33 Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.” 34 Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata. 35 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa. 36 Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? 37 Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake? 38 Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”

In Other Versions

Mark 8 in the ANGEFD

Mark 8 in the ANTPNG2D

Mark 8 in the AS21

Mark 8 in the BAGH

Mark 8 in the BBPNG

Mark 8 in the BBT1E

Mark 8 in the BDS

Mark 8 in the BEV

Mark 8 in the BHAD

Mark 8 in the BIB

Mark 8 in the BLPT

Mark 8 in the BNT

Mark 8 in the BNTABOOT

Mark 8 in the BNTLV

Mark 8 in the BOATCB

Mark 8 in the BOATCB2

Mark 8 in the BOBCV

Mark 8 in the BOCNT

Mark 8 in the BOECS

Mark 8 in the BOHCB

Mark 8 in the BOHCV

Mark 8 in the BOHLNT

Mark 8 in the BOHNTLTAL

Mark 8 in the BOICB

Mark 8 in the BOILNTAP

Mark 8 in the BOITCV

Mark 8 in the BOKCV

Mark 8 in the BOKCV2

Mark 8 in the BOKHWOG

Mark 8 in the BOKSSV

Mark 8 in the BOLCB

Mark 8 in the BOLCB2

Mark 8 in the BOMCV

Mark 8 in the BONAV

Mark 8 in the BONCB

Mark 8 in the BONLT

Mark 8 in the BONUT2

Mark 8 in the BOPLNT

Mark 8 in the BOSCB

Mark 8 in the BOSNC

Mark 8 in the BOTLNT

Mark 8 in the BOVCB

Mark 8 in the BOYCB

Mark 8 in the BPBB

Mark 8 in the BPH

Mark 8 in the BSB

Mark 8 in the CCB

Mark 8 in the CUV

Mark 8 in the CUVS

Mark 8 in the DBT

Mark 8 in the DGDNT

Mark 8 in the DHNT

Mark 8 in the DNT

Mark 8 in the ELBE

Mark 8 in the EMTV

Mark 8 in the ESV

Mark 8 in the FBV

Mark 8 in the FEB

Mark 8 in the GGMNT

Mark 8 in the GNT

Mark 8 in the HARY

Mark 8 in the HNT

Mark 8 in the IRVA

Mark 8 in the IRVB

Mark 8 in the IRVG

Mark 8 in the IRVH

Mark 8 in the IRVK

Mark 8 in the IRVM

Mark 8 in the IRVM2

Mark 8 in the IRVO

Mark 8 in the IRVP

Mark 8 in the IRVT

Mark 8 in the IRVT2

Mark 8 in the IRVU

Mark 8 in the ISVN

Mark 8 in the JSNT

Mark 8 in the KAPI

Mark 8 in the KBT1ETNIK

Mark 8 in the KBV

Mark 8 in the KJV

Mark 8 in the KNFD

Mark 8 in the LBA

Mark 8 in the LBLA

Mark 8 in the LNT

Mark 8 in the LSV

Mark 8 in the MAAL

Mark 8 in the MBV

Mark 8 in the MBV2

Mark 8 in the MHNT

Mark 8 in the MKNFD

Mark 8 in the MNG

Mark 8 in the MNT

Mark 8 in the MNT2

Mark 8 in the MRS1T

Mark 8 in the NAA

Mark 8 in the NASB

Mark 8 in the NBLA

Mark 8 in the NBS

Mark 8 in the NBVTP

Mark 8 in the NET2

Mark 8 in the NIV11

Mark 8 in the NNT

Mark 8 in the NNT2

Mark 8 in the NNT3

Mark 8 in the PDDPT

Mark 8 in the PFNT

Mark 8 in the RMNT

Mark 8 in the SBIAS

Mark 8 in the SBIBS

Mark 8 in the SBIBS2

Mark 8 in the SBICS

Mark 8 in the SBIDS

Mark 8 in the SBIGS

Mark 8 in the SBIHS

Mark 8 in the SBIIS

Mark 8 in the SBIIS2

Mark 8 in the SBIIS3

Mark 8 in the SBIKS

Mark 8 in the SBIKS2

Mark 8 in the SBIMS

Mark 8 in the SBIOS

Mark 8 in the SBIPS

Mark 8 in the SBISS

Mark 8 in the SBITS

Mark 8 in the SBITS2

Mark 8 in the SBITS3

Mark 8 in the SBITS4

Mark 8 in the SBIUS

Mark 8 in the SBIVS

Mark 8 in the SBT

Mark 8 in the SBT1E

Mark 8 in the SCHL

Mark 8 in the SNT

Mark 8 in the SUSU

Mark 8 in the SUSU2

Mark 8 in the SYNO

Mark 8 in the TBIAOTANT

Mark 8 in the TBT1E

Mark 8 in the TBT1E2

Mark 8 in the TFTIP

Mark 8 in the TFTU

Mark 8 in the TGNTATF3T

Mark 8 in the THAI

Mark 8 in the TNFD

Mark 8 in the TNT

Mark 8 in the TNTIK

Mark 8 in the TNTIL

Mark 8 in the TNTIN

Mark 8 in the TNTIP

Mark 8 in the TNTIZ

Mark 8 in the TOMA

Mark 8 in the TTENT

Mark 8 in the UBG

Mark 8 in the UGV

Mark 8 in the UGV2

Mark 8 in the UGV3

Mark 8 in the VBL

Mark 8 in the VDCC

Mark 8 in the YALU

Mark 8 in the YAPE

Mark 8 in the YBVTP

Mark 8 in the ZBP