Psalms 37 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. 1 Usamavutike chifukwa cha anthu oyipakapena kuchitira nsanje amene akuchita cholakwa; 2 pakuti monga udzu iwo adzafota msanga,ngati mbewu zobiriwira adzanyala msanga. 3 Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino;khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika. 4 Udzikondweretse wekha mwa Yehovandipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako. 5 Pereka njira yako kwa Yehova;dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi: 6 Iye adzachititsa chilungamo chako kuwala ngati mʼbandakucha,chiweruzo chako ngati dzuwa la masana. 7 Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa;usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo,pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa. 8 Pewa kupsa mtima ndipo tembenuka kuchoka ku ukali,usavutike chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoyipa. 9 Pakuti anthu oyipa adzachotsedwa,koma iwo amene amayembekeza mwa Yehova adzalandira dziko. 10 Kwa kanthawi oyipa sadzapezekanso;ngakhale muwafunefune, sadzapezekanso. 11 Koma ofatsa adzalandira dzikondipo adzasangalala ndi mtendere waukulu. 12 Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungamandipo amawakukutira mano; 13 koma Ambuye amaseka oyipapakuti Iye amadziwa kuti tsiku lawo likubwera. 14 Oyipa amasolola lupangandi kupinda utakugwetsa osauka ndi osowa,kupha iwo amene njira zawo ndi zolungama. 15 Koma malupanga awo analasa mitima yawo yomwe,ndipo mauta awo anathyoka. 16 Zabwino zochepa zimene olungama ali nazoziposa chuma cha anthu oyipa ambiri; 17 pakuti mphamvu ya oyipa idzasweka,koma Yehova amasunga olungama. 18 Masiku a anthu osalakwa amadziwika ndi Yehova,ndipo cholowa chawo chidzakhala mpaka muyaya. 19 Pa nthawi ya mavuto iwo sadzafota;mʼmasiku a njala adzakhala ndi zinthu zambiri. 20 Koma oyipa adzawonongeka;adani a Yehova adzakhala ngati kukongola kwa kuthengo,iwo adzazimirira ngati utsi. 21 Oyipa amabwereka ndipo sabwezakoma olungama amapereka mowolowamanja. 22 Iwo amene Yehova amawadalitsa adzalandira dziko,koma amene Iye amawatemberera adzachotsedwa. 23 Ngati Yehova akondwera ndi njira ya munthu,amakhazikitsa mayendedwe ake; 24 ngakhale atapunthwa sadzagwa,pakuti Yehova amamutchinjiriza ndi dzanja lake. 25 Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalambakoma sindinaonepo olungama akusiyidwakapena ana awo akupempha chakudya. 26 Iwo ndi owolowamanja nthawi zonse ndipo amabwereketsa mwaufulu;ana awo adzadalitsika. 27 Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino;pamenepo udzakhazikika mʼdziko kwamuyaya. 28 Pakuti Yehova amakonda wolungamandipo sadzasiya okhulupirika ake. Iwo adzatetezedwa kwamuyaya,koma zidzukulu za oyipa zidzachotsedwa; 29 olungama adzalandira dzikondipo adzakhazikikamo kwamuyaya. 30 Pakamwa pa munthu wolungama pamayankhula za nzeru,ndipo lilime lake limayankhula zolungama. 31 Lamulo la Mulungu wake lili mu mtima mwake;mapazi ake saterereka. 32 Oyipa amabisala kudikira olungama;kufunafuna miyoyo yawoyo; 33 koma Yehova sadzawasiya pansi pa mphamvu yawokapena kuti atsutsidwe pamene abweretsedwa pa milandu. 34 Khulupirira Yehova,ndipo sunga njira yake;Iye adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako;udzaona anthu oyipa akuwonongeka. 35 Ine ndinaona munthu woyipa ndi munthu wopanda chifundoakupeza bwino ngati mtengo wobiriwira pa nthaka ya makolo ake. 36 Koma sanachedwe kumwalira ndipo sanaonekenso;ngakhale ndinamuyangʼanayangʼana, sanapezekenso. 37 Ganizira za munthu wosalakwa, yangʼanitsitsa munthu wolungama;udzaona kuti ali ndi tsogolo labwino ndipo ali ndi zidzukulu zambiri. 38 Koma anthu ochimwa adzawonongeka;iwowo pamodzi ndi zidzukulu zawo zomwe. 39 Chipulumutso cha olungama chimachokera kwa Yehova;Iye ndiye linga lawo pa nthawi ya masautso. 40 Yehova amawathandiza ndi kuwalanditsa;Iye amawalanditsa kwa oyipa ndi kuwapulumutsa,pakuti amathawira kwa Iye.