Romans 7 (BOGWICC)

1 Kodi simukudziwa abale kuti Malamulo ali ndi ulamuliro pa munthu pokhapokha ngati ali ndi moyo? Ine ndikuyankhula kwa anthu amene akudziwa Malamulo. 2 Mwachitsanzo, Malamulo amati mkazi wokwatiwa ndi womangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wakeyo nthawi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma ngati mwamuna wake amwalira, mkaziyo ndi womasulidwa ku lamulo la ukwati. 3 Koma ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina pamene mwamuna wake ali moyo, amatchedwa wachigololo. Koma ngati mwamuna wakeyo amwalira, mkaziyo amasuka ku lamulo ndipo si wachigololo, ngakhale kuti wakwatiwa ndi mwamuna wina. 4 Chimodzimodzi inunso, abale anga, munafa ku Malamulo kudzera mʼthupi la Khristu, kuti mukwatiwe ndi wina, ndi Iye amene anauka kwa akufa kuti tibalire Mulungu chipatso. 5 Pakuti pamene tinkalamulidwa ndi khalidwe lathu lauchimo, zilakolako zauchimo zimene Malamulo anaziwutsa zinkagwira ntchito mʼmatupi mwathu kotero kuti zinabala imfa. 6 Koma tsopano tamasulidwa ku Malamulowo pakuti tinafa ku zimene zinkatimanga, ndipo Mzimu Woyera akutithandiza kutumikira Mulungu mʼnjira yatsopano ndipo osati mʼnjira yakale yolembedwa. 7 Nanga ife tinene chiyani? Kodi Malamulo ndi oyipa? Ayi. Nʼkosatheka! Kunena zoona, popanda Malamulo, ine sindikanazindikira tchimo. Pakuti sindikanadziwa kuti kusirira ndi tchimo ngati Malamulo sakananena kuti, “Usasirire.” 8 Koma chifukwa cha Malamulo uchimo unapeza mwayi owutsa mʼkati mwanga khalidwe lililonse la kusirira. Pakuti pakanapanda Malamulo, uchimo ukanakhala wopanda mphamvu. 9 Nthawi ina ndinali ndi moyo popanda Malamulo. Koma nditayamba kudziwa Malamulo, pomwepo uchimo unayamba kuphuka, 10 ndipo ine ndinafa. Ine ndinazindikira kuti Malamulo omwe ankayenera kubweretsa moyo anabweretsa imfa. 11 Pakuti uchimo unapeza mwayi chifukwa cha Malamulo ndipo kudzera mʼMalamulowo, unandinyenga ndi kundiyika mu imfa. 12 Choncho lamulo ndi loyera, lolungama ndi labwino. 13 Kodi chomwe ndi chabwino tsopano chinasanduka imfa kwa ine? Si choncho ayi! Koma kuti uchimo uzindikirike kuti ndi uchimo unabala imfa mwa ine kudzera mu chomwe chinali chabwino, kotero kuti kudzera mu lamulo uchimo ukhale oyipa kopitirira. 14 Ife tikudziwa kuti Malamulo ndi auzimu; koma ine ndine munthu wofowoka chabe, wogulitsidwa ngati kapolo ku uchimo. 15 Ine sindizindikira zimene ndimachita. Pakuti zimene ndimafuna kuchita sindizichita koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimazichita. 16 Ndipo ngati ndimachita zimene sindimafuna kuzichita, ndiye kuti ndikuvomereza kuti lamulo ndi labwino. 17 Monga mmene zililimu, si inenso mwini amene ndimazichita zimenezi, koma tchimo limene lili mʼkati mwanga. 18 Ine ndikudziwa kuti mwa ine mulibe kanthu kabwino, ndiye kuti mʼthupi langa lauchimo. Pakuti ndimafuna kuchita zabwino, koma ndimalephera kuzichita. 19 Ine sindichita zabwino zimene ndimafuna koma ndimachita zonyansa zimene sindikuzifuna. 20 Tsopano ngati ine ndimachita zimene sindikuzifuna, si inenso amene ndimazichita, koma ndi tchimo limene lili mʼkati mwanga. 21 Tsono ndapeza kuti lamuloli likugwira ntchito. Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino, zoyipa zili nane pomwepo. 22 Mtima wanga umakondwera ndi lamulo la Mulungu. 23 Koma mʼkati mwanga ndimaona lamulo lina likugwira ntchito kulimbana ndi zomwe mtima wanga umavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa wamʼndende walamulo la uchimo lomwe likugwira ntchito mʼkati mwa ziwalo zanga. 24 Kalanga ine! Adzandipulumutsa ndani ku thupi la imfali? 25 Atamandike Mulungu, amene amandipulumutsa kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu!Kotero tsono, ineyo ndi mtima wanga ndimatumikira lamulo la Mulungu, koma ndi thupi langa ndimatumikira lamulo la uchimo.

In Other Versions

Romans 7 in the ANGEFD

Romans 7 in the ANTPNG2D

Romans 7 in the AS21

Romans 7 in the BAGH

Romans 7 in the BBPNG

Romans 7 in the BBT1E

Romans 7 in the BDS

Romans 7 in the BEV

Romans 7 in the BHAD

Romans 7 in the BIB

Romans 7 in the BLPT

Romans 7 in the BNT

Romans 7 in the BNTABOOT

Romans 7 in the BNTLV

Romans 7 in the BOATCB

Romans 7 in the BOATCB2

Romans 7 in the BOBCV

Romans 7 in the BOCNT

Romans 7 in the BOECS

Romans 7 in the BOHCB

Romans 7 in the BOHCV

Romans 7 in the BOHLNT

Romans 7 in the BOHNTLTAL

Romans 7 in the BOICB

Romans 7 in the BOILNTAP

Romans 7 in the BOITCV

Romans 7 in the BOKCV

Romans 7 in the BOKCV2

Romans 7 in the BOKHWOG

Romans 7 in the BOKSSV

Romans 7 in the BOLCB

Romans 7 in the BOLCB2

Romans 7 in the BOMCV

Romans 7 in the BONAV

Romans 7 in the BONCB

Romans 7 in the BONLT

Romans 7 in the BONUT2

Romans 7 in the BOPLNT

Romans 7 in the BOSCB

Romans 7 in the BOSNC

Romans 7 in the BOTLNT

Romans 7 in the BOVCB

Romans 7 in the BOYCB

Romans 7 in the BPBB

Romans 7 in the BPH

Romans 7 in the BSB

Romans 7 in the CCB

Romans 7 in the CUV

Romans 7 in the CUVS

Romans 7 in the DBT

Romans 7 in the DGDNT

Romans 7 in the DHNT

Romans 7 in the DNT

Romans 7 in the ELBE

Romans 7 in the EMTV

Romans 7 in the ESV

Romans 7 in the FBV

Romans 7 in the FEB

Romans 7 in the GGMNT

Romans 7 in the GNT

Romans 7 in the HARY

Romans 7 in the HNT

Romans 7 in the IRVA

Romans 7 in the IRVB

Romans 7 in the IRVG

Romans 7 in the IRVH

Romans 7 in the IRVK

Romans 7 in the IRVM

Romans 7 in the IRVM2

Romans 7 in the IRVO

Romans 7 in the IRVP

Romans 7 in the IRVT

Romans 7 in the IRVT2

Romans 7 in the IRVU

Romans 7 in the ISVN

Romans 7 in the JSNT

Romans 7 in the KAPI

Romans 7 in the KBT1ETNIK

Romans 7 in the KBV

Romans 7 in the KJV

Romans 7 in the KNFD

Romans 7 in the LBA

Romans 7 in the LBLA

Romans 7 in the LNT

Romans 7 in the LSV

Romans 7 in the MAAL

Romans 7 in the MBV

Romans 7 in the MBV2

Romans 7 in the MHNT

Romans 7 in the MKNFD

Romans 7 in the MNG

Romans 7 in the MNT

Romans 7 in the MNT2

Romans 7 in the MRS1T

Romans 7 in the NAA

Romans 7 in the NASB

Romans 7 in the NBLA

Romans 7 in the NBS

Romans 7 in the NBVTP

Romans 7 in the NET2

Romans 7 in the NIV11

Romans 7 in the NNT

Romans 7 in the NNT2

Romans 7 in the NNT3

Romans 7 in the PDDPT

Romans 7 in the PFNT

Romans 7 in the RMNT

Romans 7 in the SBIAS

Romans 7 in the SBIBS

Romans 7 in the SBIBS2

Romans 7 in the SBICS

Romans 7 in the SBIDS

Romans 7 in the SBIGS

Romans 7 in the SBIHS

Romans 7 in the SBIIS

Romans 7 in the SBIIS2

Romans 7 in the SBIIS3

Romans 7 in the SBIKS

Romans 7 in the SBIKS2

Romans 7 in the SBIMS

Romans 7 in the SBIOS

Romans 7 in the SBIPS

Romans 7 in the SBISS

Romans 7 in the SBITS

Romans 7 in the SBITS2

Romans 7 in the SBITS3

Romans 7 in the SBITS4

Romans 7 in the SBIUS

Romans 7 in the SBIVS

Romans 7 in the SBT

Romans 7 in the SBT1E

Romans 7 in the SCHL

Romans 7 in the SNT

Romans 7 in the SUSU

Romans 7 in the SUSU2

Romans 7 in the SYNO

Romans 7 in the TBIAOTANT

Romans 7 in the TBT1E

Romans 7 in the TBT1E2

Romans 7 in the TFTIP

Romans 7 in the TFTU

Romans 7 in the TGNTATF3T

Romans 7 in the THAI

Romans 7 in the TNFD

Romans 7 in the TNT

Romans 7 in the TNTIK

Romans 7 in the TNTIL

Romans 7 in the TNTIN

Romans 7 in the TNTIP

Romans 7 in the TNTIZ

Romans 7 in the TOMA

Romans 7 in the TTENT

Romans 7 in the UBG

Romans 7 in the UGV

Romans 7 in the UGV2

Romans 7 in the UGV3

Romans 7 in the VBL

Romans 7 in the VDCC

Romans 7 in the YALU

Romans 7 in the YAPE

Romans 7 in the YBVTP

Romans 7 in the ZBP