Acts 25 (BOGWICC)

1 Patapita masiku atatu Festo atafika mʼdera lake, anachoka ku Kaisareya ndi kupita ku Yerusalemu. 2 Kumeneko akulu a ansembe ndi atsogoleri a Chiyuda anabwera kwa iye ndi kumufotokozera mlandu wa Paulo. 3 Iwo anamupempha Festo kuti awakomere mtima potumiza Paulo ku Yerusalemu, pakuti anali atakonzekera chiwembu kuti amuphe Pauloyo pa njira. 4 Festo anayankha kuti, “Paulo akusungidwa ku Kaisareya, ndipo ndipita kumeneko posachedwa. 5 Ena mwa atsogoleri anu apite nane kumeneko, kuti akafotokoze mlandu wa munthuyu, ngati anachita kanthu kalikonse kolakwika.” 6 Festo atakhala nawo masiku asanu ndi atatu kapena khumi iye anapita ku Kaisareya, ndipo mmawa mwake anayitanitsa bwalo nalamula kuti abweretse Paulo pamaso pake. 7 Paulo atafika, Ayuda amene anafika kuchokera ku Yerusalemu anayima momuzungulira. Iwo anamunenera zinthu zoopsa zambiri zimene sakanatha kubweretsa umboni wake. 8 Kenaka Paulo ananena mawu ake odziteteza kuti, “Ine sindinalakwirepo lamulo la Ayuda, kapena Nyumba ya Mulungu kapenanso Kaisara.” 9 Festo, pofuna kuti Ayuda amukonde anafunsa Paulo kuti, “Kodi iwe ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti kumeneko ukafotokoze mlandu wako pamaso panga?” 10 Paulo anayankha kuti, “Ine tsopano ndayima pamaso pa bwalo la milandu la Kaisara, ndiko kumene ayenera kundiweruza. Ine sindinalakwire Ayuda, monga inu mukudziwa bwino. 11 Koma ngati ndili wolakwa, ngati ndachita kanthu koyenera kuphedwa, ine sindikukana kufa. Koma ngati mlandu umene abweretsa Ayudawa siwoona, palibe munthu angathe kundipereka mʼmanja mwawo. Ndikupempha kuti ndikaweruzidwe ndi Kaisara!” 12 Festo atakambirana ndi akuluakulu abwalo lake, anati, “Popeza wapempha kupita kwa Kaisara, kwa Kaisara udzapitadi!” 13 Patapita masiku ochepa mfumu Agripa pamodzi ndi Bernisi anabwera ku Kaisareya kudzalonjera Festo. 14 Atakhala kumeneko masiku angapo, Festo anafotokozera mfumuyo za mlandu wa Paulo. Iye anati, “Kuli munthu wina kuno amene Felike anamusiya mʼndende. 15 Nditapita ku Yerusalemu akulu a ansembe ndi akuluakulu a Ayuda anandifotokozera mlandu wake ndipo anandipempha kuti ndigamule kuti ndi wolakwa. 16 “Ine ndinawayankha kuti si mwambo wa Aroma kungomupereka munthu ayi. Munthu woyimbidwa mlanduyo amayenera kukumana nawo omunenezawo, kuti iye akhale ndi mwayi woyankhapo pa zimene akumuyimba mlanduzo. 17 Atabwera kuno pamodzi ndi ine, sindinachedwetse mlanduwo, koma ndinayitanitsa bwalo mmawa mwake ndi kulamula kuti amubweretse munthuyo. 18 Omuyimba mlandu aja atayimirira kuti ayankhule, iwo sananene cholakwa chilichonse chimene ndimayembekezera. 19 Mʼmalo mwake, anatsutsana naye pa fundo zina za chipembedzo chawo ndi za munthu wakufa, dzina lake Yesu, amene Paulo akuti ali moyo. 20 Ine ndinathedwa nzeru wosadziwa momwe ndikanafufuzira nkhaniyi; kotero ndinafunsa ngati akanafuna kupita ku Yerusalemu kuti akaweruzidwe kumeneko. 21 Koma Paulo anapempha kuti akaonekere pamaso pa mfumu ya Chiroma, ndipo ndinalamula kuti asungidwe mpaka pamene ndidzamutumize kwa Kaisara.” 22 Ndipo Agripa anati kwa Festo, “Ine ndikufuna ndimumve ndekha munthu ameneyu.” Iye anayankha kuti, “Mudzamumva mawa.” 23 Mmawa mwake Agripa ndi Bernisi anabwera mwaulemu waukulu waufumu nalowa mʼbwalo la milandu pamodzi ndi akulu a asilikali ndiponso akuluakulu a mu mzindawo. Atalamula Festo kuti Paulo abwere, anabweradi. 24 Festo anati, “Mfumu Agripa, ndi onse amene muli nafe pano, mukumuona munthu uyu! Ayuda onse anandipempha ine za uyu ku Yerusalemu ndiponso kuno ku Kaisareya, mofuwula kuti, ameneyu sayenera kukhala ndi moyo. 25 Ine ndinapeza kuti iyeyu sanachite kanthu koyenera kufa, koma popeza anapempha kuti apite kwa mfumu ya Chiroma, ine ndinatsimikiza zomutumiza ku Roma. 26 Koma ndilibe kanthu kenikeni koti ndilembere Wolemekezekayo za iyeyu. Nʼchifukwa chake ndabwera naye pamaso pa nonsenu, makamaka kwa inuyo mfumu Agripa, kuti mwina mukamufunsitsa ndikhale ndi choti ndilembe. 27 Pakuti ine ndikuganiza kuti ndi chinthu chopanda nzeru kutumiza wamʼndende popanda kutchula zifukwa zenizeni za mlandu wake.”

In Other Versions

Acts 25 in the ANGEFD

Acts 25 in the ANTPNG2D

Acts 25 in the AS21

Acts 25 in the BAGH

Acts 25 in the BBPNG

Acts 25 in the BBT1E

Acts 25 in the BDS

Acts 25 in the BEV

Acts 25 in the BHAD

Acts 25 in the BIB

Acts 25 in the BLPT

Acts 25 in the BNT

Acts 25 in the BNTABOOT

Acts 25 in the BNTLV

Acts 25 in the BOATCB

Acts 25 in the BOATCB2

Acts 25 in the BOBCV

Acts 25 in the BOCNT

Acts 25 in the BOECS

Acts 25 in the BOHCB

Acts 25 in the BOHCV

Acts 25 in the BOHLNT

Acts 25 in the BOHNTLTAL

Acts 25 in the BOICB

Acts 25 in the BOILNTAP

Acts 25 in the BOITCV

Acts 25 in the BOKCV

Acts 25 in the BOKCV2

Acts 25 in the BOKHWOG

Acts 25 in the BOKSSV

Acts 25 in the BOLCB

Acts 25 in the BOLCB2

Acts 25 in the BOMCV

Acts 25 in the BONAV

Acts 25 in the BONCB

Acts 25 in the BONLT

Acts 25 in the BONUT2

Acts 25 in the BOPLNT

Acts 25 in the BOSCB

Acts 25 in the BOSNC

Acts 25 in the BOTLNT

Acts 25 in the BOVCB

Acts 25 in the BOYCB

Acts 25 in the BPBB

Acts 25 in the BPH

Acts 25 in the BSB

Acts 25 in the CCB

Acts 25 in the CUV

Acts 25 in the CUVS

Acts 25 in the DBT

Acts 25 in the DGDNT

Acts 25 in the DHNT

Acts 25 in the DNT

Acts 25 in the ELBE

Acts 25 in the EMTV

Acts 25 in the ESV

Acts 25 in the FBV

Acts 25 in the FEB

Acts 25 in the GGMNT

Acts 25 in the GNT

Acts 25 in the HARY

Acts 25 in the HNT

Acts 25 in the IRVA

Acts 25 in the IRVB

Acts 25 in the IRVG

Acts 25 in the IRVH

Acts 25 in the IRVK

Acts 25 in the IRVM

Acts 25 in the IRVM2

Acts 25 in the IRVO

Acts 25 in the IRVP

Acts 25 in the IRVT

Acts 25 in the IRVT2

Acts 25 in the IRVU

Acts 25 in the ISVN

Acts 25 in the JSNT

Acts 25 in the KAPI

Acts 25 in the KBT1ETNIK

Acts 25 in the KBV

Acts 25 in the KJV

Acts 25 in the KNFD

Acts 25 in the LBA

Acts 25 in the LBLA

Acts 25 in the LNT

Acts 25 in the LSV

Acts 25 in the MAAL

Acts 25 in the MBV

Acts 25 in the MBV2

Acts 25 in the MHNT

Acts 25 in the MKNFD

Acts 25 in the MNG

Acts 25 in the MNT

Acts 25 in the MNT2

Acts 25 in the MRS1T

Acts 25 in the NAA

Acts 25 in the NASB

Acts 25 in the NBLA

Acts 25 in the NBS

Acts 25 in the NBVTP

Acts 25 in the NET2

Acts 25 in the NIV11

Acts 25 in the NNT

Acts 25 in the NNT2

Acts 25 in the NNT3

Acts 25 in the PDDPT

Acts 25 in the PFNT

Acts 25 in the RMNT

Acts 25 in the SBIAS

Acts 25 in the SBIBS

Acts 25 in the SBIBS2

Acts 25 in the SBICS

Acts 25 in the SBIDS

Acts 25 in the SBIGS

Acts 25 in the SBIHS

Acts 25 in the SBIIS

Acts 25 in the SBIIS2

Acts 25 in the SBIIS3

Acts 25 in the SBIKS

Acts 25 in the SBIKS2

Acts 25 in the SBIMS

Acts 25 in the SBIOS

Acts 25 in the SBIPS

Acts 25 in the SBISS

Acts 25 in the SBITS

Acts 25 in the SBITS2

Acts 25 in the SBITS3

Acts 25 in the SBITS4

Acts 25 in the SBIUS

Acts 25 in the SBIVS

Acts 25 in the SBT

Acts 25 in the SBT1E

Acts 25 in the SCHL

Acts 25 in the SNT

Acts 25 in the SUSU

Acts 25 in the SUSU2

Acts 25 in the SYNO

Acts 25 in the TBIAOTANT

Acts 25 in the TBT1E

Acts 25 in the TBT1E2

Acts 25 in the TFTIP

Acts 25 in the TFTU

Acts 25 in the TGNTATF3T

Acts 25 in the THAI

Acts 25 in the TNFD

Acts 25 in the TNT

Acts 25 in the TNTIK

Acts 25 in the TNTIL

Acts 25 in the TNTIN

Acts 25 in the TNTIP

Acts 25 in the TNTIZ

Acts 25 in the TOMA

Acts 25 in the TTENT

Acts 25 in the UBG

Acts 25 in the UGV

Acts 25 in the UGV2

Acts 25 in the UGV3

Acts 25 in the VBL

Acts 25 in the VDCC

Acts 25 in the YALU

Acts 25 in the YAPE

Acts 25 in the YBVTP

Acts 25 in the ZBP