Deuteronomy 22 (BOGWICC)

1 Ngati uwona ngʼombe kapena nkhosa ya mʼbale wako ikusochera, usayilekerere koma uyesetse kuyibwezera kwa iye. 2 Ngati mʼbale wakoyo sakhala pafupi kapena sukudziwa kuti ndi yandani, uyitengere ku nyumba kwako ndi kuyisamala mpaka mwini wake atayilondola ndipo umubwezere. 3 Uzitero ndithu ngati upeza bulu kapena mkanjo kapena chilichonse chimene chatayika. Osachilekerera. 4 Ngati wapeza bulu kapena ngʼombe ya mʼbale wako itagwa panjira, usayilekerere. Ithandize kuti idzuke. 5 Akazi asavale zovala za amuna, kapena mwamuna kuvala zovala za akazi, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita izi. 6 Ukapeza chisa cha mbalame mʼmphepete mwa msewu, kaya ndi mu mtengo kapena pansi, mbalame yayikazi itafungatira ana kapena mazira, usatenge mbalameyo pamodzi ndi ana ake omwe. 7 Anawo mukhoza kutenga koma onetsetsani kuti mayi wawo mwamutaya kuti apite, kuti zinthu zizikuyenderani bwino ndiponso kuti mukhale ndi moyo wautali. 8 Mukamanga nyumba yatsopano, mutchingire khonde lake la pa denga kuti inu musapezeke ndi mlandu wopha munthu ngati wina agwa kuchokera pa khonde la pa dengalo. 9 Musadzale mbewu zamitundu iwiri mʼmunda wanu wa mpesa, ngati mutero, si mbewu zanu zokha zimene zidzakhale zodetsedwa, komanso zipatso za mʼmunda wamphesawo. 10 Musatipule pogwiritsa ntchito ngʼombe ndi bulu pa goli limodzi. 11 Musamavale chovala chopangidwa mophatikiza ubweya ndi thonje. 12 Muzipanga mphonje mʼngodya za mkanjo umene mumavala. 13 Ngati munthu akwatira mkazi, ndipo atagona naye nʼkusamufunanso 14 namunyoza ndi kumuyipitsira dzina nʼkumati, “Ine ndinakwatira mkazi uyu, koma pamene ndinakhala naye, sindinachione chizindikiro cha unamwali wake,” 15 zikatero abambo ndi amayi ake ayenera kubweretsa chitsimikizo chakuti anali namwali kwa akuluakulu a mzinda ku chipata. 16 Abambo ake a mtsikanayo adzanene kwa akuluakuluwo kuti, “Ine ndinamupatsa munthu uyu mwana wanga wamkazi kuti amukwatire, koma sakumufunanso. 17 Tsopano wamunyoza ndipo wanena kuti, ‘Ine sindinapeze kuti mwana wanu wamkaziyu ndi namwali.’ Koma tsopano onani chitsimikizo ichi cha unamwali wa mwana wanga wamkazi.” Kenaka makolo a mtsikanayo adzaonetse kansalu kwa akuluakulu aja, 18 ndipo akuluakuluwo adzamugwire munthuyo namupatsa chilango. 19 Iwo adzamulipitse ndalama zasiliva zokwana 100 nazipereka kwa abambo a mtsikana, chifukwa munthu uyu wayipitsa dzina la mtsikana wa Chiisraeli. Ayenera kukhalabe mkazi wake ndipo asadzamuleke moyo wake wonse. 20 Koma ngati zomunenerazo ndi zoona, ndipo kuti chitsimikizo cha unamwali wa mtsikanayo sichinapezeke, 21 iyeyu ayenera kumutengera pa khomo pa abambo ake pamene anthu a mu mzinda wake akamuphere ndi miyala. Iyeyo wachita chinthu chochititsa manyazi mu Israeli pochita chiwerewere akanali pa khomo pa abambo ake. Muyenera kuchotsa zoyipa pakati panu. 22 Ngati munthu apezeka akugona ndi mkazi wa mwini wake, ayenera kuphedwa munthuyo pamodzi ndi mkazi yemwe wagona nayeyo. Muyenera kuchotsa zoyipa mu Israeli. 23 Ngati munthu mu mzinda akumana ndi mkazi yemwe anachita kale chinkhoswe nagona naye, 24 muwatengere awiriwo ku chipata cha mzinda ndi kuwapha ndi miyala. Aphedwe chifukwa mtsikanayo anali pafupi ndi anthu ndipo sanakuwe kuti ena amuthandize ndipo mwamunayo chifukwa anayipitsa mkazi wa mwini. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu. 25 Koma ngati munthu akumana ndi mkazi kutchire yemwe anachita kale chinkhoswe namugwiririra, mwamuna yekhayo ndiye woyenera kuphedwa. 26 Mtsikanayo musamuchite chilichonse, palibe tchimo limene wachita loti ayenera kuphedwa. Mlandu uwu ufanana ndi wa munthu amene alimbana ndi kupha mnzake woyandikana naye, 27 pakuti mwamunayo anamupeza mtsikanayo kutchire, ndipo ngakhale mtsikana wachinkhosweyo anakuwa, panalibe anamulanditsa. 28 Ngati munthu apezana ndi namwali woti sanachite chinkhoswe, namugwiririra, munthuyo nʼkupezeka, 29 ayenera kuwalipira abambo ake a namwaliyo ndalama za siliva makumi asanu. Iye ayenera kumukwatira mkaziyo chifukwa wamuyipitsa, ndipo sadzamulekanso moyo wake wonse. 30 Munthu asakwatire mkazi wa abambo ake pakuti ayenera kuchitira ulemu pogona pa abambo ake.

In Other Versions

Deuteronomy 22 in the ANGEFD

Deuteronomy 22 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 22 in the AS21

Deuteronomy 22 in the BAGH

Deuteronomy 22 in the BBPNG

Deuteronomy 22 in the BBT1E

Deuteronomy 22 in the BDS

Deuteronomy 22 in the BEV

Deuteronomy 22 in the BHAD

Deuteronomy 22 in the BIB

Deuteronomy 22 in the BLPT

Deuteronomy 22 in the BNT

Deuteronomy 22 in the BNTABOOT

Deuteronomy 22 in the BNTLV

Deuteronomy 22 in the BOATCB

Deuteronomy 22 in the BOATCB2

Deuteronomy 22 in the BOBCV

Deuteronomy 22 in the BOCNT

Deuteronomy 22 in the BOECS

Deuteronomy 22 in the BOHCB

Deuteronomy 22 in the BOHCV

Deuteronomy 22 in the BOHLNT

Deuteronomy 22 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 22 in the BOICB

Deuteronomy 22 in the BOILNTAP

Deuteronomy 22 in the BOITCV

Deuteronomy 22 in the BOKCV

Deuteronomy 22 in the BOKCV2

Deuteronomy 22 in the BOKHWOG

Deuteronomy 22 in the BOKSSV

Deuteronomy 22 in the BOLCB

Deuteronomy 22 in the BOLCB2

Deuteronomy 22 in the BOMCV

Deuteronomy 22 in the BONAV

Deuteronomy 22 in the BONCB

Deuteronomy 22 in the BONLT

Deuteronomy 22 in the BONUT2

Deuteronomy 22 in the BOPLNT

Deuteronomy 22 in the BOSCB

Deuteronomy 22 in the BOSNC

Deuteronomy 22 in the BOTLNT

Deuteronomy 22 in the BOVCB

Deuteronomy 22 in the BOYCB

Deuteronomy 22 in the BPBB

Deuteronomy 22 in the BPH

Deuteronomy 22 in the BSB

Deuteronomy 22 in the CCB

Deuteronomy 22 in the CUV

Deuteronomy 22 in the CUVS

Deuteronomy 22 in the DBT

Deuteronomy 22 in the DGDNT

Deuteronomy 22 in the DHNT

Deuteronomy 22 in the DNT

Deuteronomy 22 in the ELBE

Deuteronomy 22 in the EMTV

Deuteronomy 22 in the ESV

Deuteronomy 22 in the FBV

Deuteronomy 22 in the FEB

Deuteronomy 22 in the GGMNT

Deuteronomy 22 in the GNT

Deuteronomy 22 in the HARY

Deuteronomy 22 in the HNT

Deuteronomy 22 in the IRVA

Deuteronomy 22 in the IRVB

Deuteronomy 22 in the IRVG

Deuteronomy 22 in the IRVH

Deuteronomy 22 in the IRVK

Deuteronomy 22 in the IRVM

Deuteronomy 22 in the IRVM2

Deuteronomy 22 in the IRVO

Deuteronomy 22 in the IRVP

Deuteronomy 22 in the IRVT

Deuteronomy 22 in the IRVT2

Deuteronomy 22 in the IRVU

Deuteronomy 22 in the ISVN

Deuteronomy 22 in the JSNT

Deuteronomy 22 in the KAPI

Deuteronomy 22 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 22 in the KBV

Deuteronomy 22 in the KJV

Deuteronomy 22 in the KNFD

Deuteronomy 22 in the LBA

Deuteronomy 22 in the LBLA

Deuteronomy 22 in the LNT

Deuteronomy 22 in the LSV

Deuteronomy 22 in the MAAL

Deuteronomy 22 in the MBV

Deuteronomy 22 in the MBV2

Deuteronomy 22 in the MHNT

Deuteronomy 22 in the MKNFD

Deuteronomy 22 in the MNG

Deuteronomy 22 in the MNT

Deuteronomy 22 in the MNT2

Deuteronomy 22 in the MRS1T

Deuteronomy 22 in the NAA

Deuteronomy 22 in the NASB

Deuteronomy 22 in the NBLA

Deuteronomy 22 in the NBS

Deuteronomy 22 in the NBVTP

Deuteronomy 22 in the NET2

Deuteronomy 22 in the NIV11

Deuteronomy 22 in the NNT

Deuteronomy 22 in the NNT2

Deuteronomy 22 in the NNT3

Deuteronomy 22 in the PDDPT

Deuteronomy 22 in the PFNT

Deuteronomy 22 in the RMNT

Deuteronomy 22 in the SBIAS

Deuteronomy 22 in the SBIBS

Deuteronomy 22 in the SBIBS2

Deuteronomy 22 in the SBICS

Deuteronomy 22 in the SBIDS

Deuteronomy 22 in the SBIGS

Deuteronomy 22 in the SBIHS

Deuteronomy 22 in the SBIIS

Deuteronomy 22 in the SBIIS2

Deuteronomy 22 in the SBIIS3

Deuteronomy 22 in the SBIKS

Deuteronomy 22 in the SBIKS2

Deuteronomy 22 in the SBIMS

Deuteronomy 22 in the SBIOS

Deuteronomy 22 in the SBIPS

Deuteronomy 22 in the SBISS

Deuteronomy 22 in the SBITS

Deuteronomy 22 in the SBITS2

Deuteronomy 22 in the SBITS3

Deuteronomy 22 in the SBITS4

Deuteronomy 22 in the SBIUS

Deuteronomy 22 in the SBIVS

Deuteronomy 22 in the SBT

Deuteronomy 22 in the SBT1E

Deuteronomy 22 in the SCHL

Deuteronomy 22 in the SNT

Deuteronomy 22 in the SUSU

Deuteronomy 22 in the SUSU2

Deuteronomy 22 in the SYNO

Deuteronomy 22 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 22 in the TBT1E

Deuteronomy 22 in the TBT1E2

Deuteronomy 22 in the TFTIP

Deuteronomy 22 in the TFTU

Deuteronomy 22 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 22 in the THAI

Deuteronomy 22 in the TNFD

Deuteronomy 22 in the TNT

Deuteronomy 22 in the TNTIK

Deuteronomy 22 in the TNTIL

Deuteronomy 22 in the TNTIN

Deuteronomy 22 in the TNTIP

Deuteronomy 22 in the TNTIZ

Deuteronomy 22 in the TOMA

Deuteronomy 22 in the TTENT

Deuteronomy 22 in the UBG

Deuteronomy 22 in the UGV

Deuteronomy 22 in the UGV2

Deuteronomy 22 in the UGV3

Deuteronomy 22 in the VBL

Deuteronomy 22 in the VDCC

Deuteronomy 22 in the YALU

Deuteronomy 22 in the YAPE

Deuteronomy 22 in the YBVTP

Deuteronomy 22 in the ZBP