Deuteronomy 33 (BOGWICC)

1 Awa ndi madalitso amene Mose, munthu wa Mulungu, anawapereka kwa Aisraeli asanafe. 2 Iye anati:“Yehova anabwera kuchokera ku Sinaindipo anatulukira kuchokera ku Seiri;anawala kuchokera pa Phiri la Parani.Iye anabwera ndi chiwunyinji cha angelokuchokera kummwera, moto woyaka uli mʼdzanja mwake. 3 Ndithu ndinu amene mumakonda anthu anu;opatulika ake onse ali mʼmanja mwake.Onse amagwada pansi pa mapazi anukuchokera kwa inu amalandira malangizo, 4 malamulo amene Mose anatipatsa,chuma chopambana cha mtundu wa Yakobo. 5 Iye anali mfumu ya Yesurunipamene atsogoleri a anthu anasonkhana,pamodzi ndi mafuko a Israeli. 6 “Lolani Rubeni akhale ndi moyo ndipo asafe,anthu ake asachepe pa chiwerengero.” 7 Ndipo ponena za Yuda anati:“Inu Yehova, imvani kulira kwa Yuda;mubweretseni kwa anthu ake.Ndi manja ake omwe adziteteze yekha.Inu khalani thandizo lake polimbana ndi adani ake!” 8 Za fuko la Alevi anati:“Tumimu wanu ndi Urimu ndi zamtumiki wanu wokhulupirika.Munamuyesa ku Masa;munalimbana naye ku madzi a ku Meriba. 9 Iye ananena za abambo ake ndi amayi ake kuti,‘Sindilabadira za iwo.’Sanasamale za abale akekapena ana ake,koma anayangʼanira mawu anundipo anateteza pangano lanu. 10 Iye amaphunzitsa Yakobo malangizo anundi malamulo anu kwa Israeli.Amafukiza lubani pamaso panundiponso amapereka nsembe zanu zonse zopsereza pa guwa lanu. 11 Inu Yehova, dalitsani luso lake lonsendipo mukondwere ndi ntchito za manja ake.Menyani adani awo mʼchiwunokanthani amene amuwukira kuti asadzukenso.” 12 Za fuko la Benjamini anati:“Wokondedwa wa Yehova akhale mwamtendere mwa Iye,pakuti amamuteteza tsiku lonse,ndipo amene Yehova amamukonda amawusa pa mapewa ake.” 13 Za fuko la Yosefe anati:“Yehova adalitse dziko lakendi mame ambiri ochokera kumwambandiponso madzi ambiri ochokera pansi pa nthaka; 14 ndi zinthu zambiri zimene zimacha ndi dzuwandiponso ndi zokolola zabwino kwambiri zimene zimacha ndi mwezi uliwonse; 15 ndi zipatso zabwino kwambiri zochokera mʼmapiri amakedzanawandiponso zokolola zochuluka zochokera ku zitunda zakalekale; 16 ndi mphatso zabwino kwambiri zochokera pa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemondiponso kukoma mtima kwa Iye amene amakhala mʼchitsamba choyaka moto.Madalitso onsewa akhale pa mutu pa Yosefe,wapaderadera pakati pa abale ake. 17 Ulemerero wake uli ngati ngʼombe yayimuna yoyamba kubadwa;nyanga zake zili ngati za njati.Ndi nyanga zakezo adzapirikitsa anthu a mitundu ina,ngakhale iwo amene akukhala ku malekezero a dziko lapansi.Nyanga zimenezi ndiye anthu miyandamiyanda a Efereimu;nyanga zimenezi ndiye anthu 1,000 a Manase.” 18 Za fuko la Zebuloni anati:“Kondwera Zebuloni, pamene ukutuluka,ndipo iwe, Isakara, kondwera mʼmatenti ako. 19 Adzayitanira mitundu ya anthu kumapiri,kumeneko adzaperekako nsembe zachilungamo;kumeneko adzadyerera zinthu zochuluka zochokera ku nyanja,chuma chobisika mu mchenga.” 20 Za fuko la Gadi anati:“Wodala amene amakulitsa malire a Gadi!Gadi amakhala kumeneko ngati mkango,kukhadzula mkono kapena mutu. 21 Iye anadzisankhira dziko labwino kwambiri;gawo la mtsogoleri anasungira iye.Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana,anachita chifuniro cha Yehova molungama,ndiponso malamulo onena za Israeli.” 22 Za fuko la Dani anati:“Dani ndi mwana wamkango,amene akutuluka ku Basani.” 23 Za fuko la Nafutali anati:“Nafutali wadzaza ndi kukoma mtima kwa Yehovandipo ndi wodzaza ndi madalitso ake;cholowa chake chidzakhala mbali ya kummwera kwa nyanja.” 24 Za fuko la Aseri anati:“Mwana wodalitsika kwambiri ndi Aseri;abale ake amukomere mtima,ndipo asambe mapazi ake mʼmafuta. 25 Zotsekera za zipata zako zidzakhala za chitsulo ndi za mkuwa,ndi mphamvu zako zidzakhala ngati masiku a moyo wako. 26 “Palibe wina wofanana ndi Mulungu wa Yesuruni,amene amakwera pa thambo kukuthandizanindiponso pa mitambo ya ulemerero wake. 27 Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu,ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha.Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu,adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’ 28 Motero Israeli adzakhala yekha mwamtendere;zidzukulu za Yakobo zili pa mtenderemʼdziko la tirigu ndi vinyo watsopano,kumene thambo limagwetsa mame. 29 Iwe Israeli, ndiwe wodala!Wofanana nanu ndanianthu opulumutsidwa ndi Yehova?Iye ndiye chishango ndi mthandizi wanundi lupanga lanu la ulemerero.Adani ako adzakugonjera,ndipo iwe udzapondereza pansi malo awo achipembedzo.”

In Other Versions

Deuteronomy 33 in the ANGEFD

Deuteronomy 33 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 33 in the AS21

Deuteronomy 33 in the BAGH

Deuteronomy 33 in the BBPNG

Deuteronomy 33 in the BBT1E

Deuteronomy 33 in the BDS

Deuteronomy 33 in the BEV

Deuteronomy 33 in the BHAD

Deuteronomy 33 in the BIB

Deuteronomy 33 in the BLPT

Deuteronomy 33 in the BNT

Deuteronomy 33 in the BNTABOOT

Deuteronomy 33 in the BNTLV

Deuteronomy 33 in the BOATCB

Deuteronomy 33 in the BOATCB2

Deuteronomy 33 in the BOBCV

Deuteronomy 33 in the BOCNT

Deuteronomy 33 in the BOECS

Deuteronomy 33 in the BOHCB

Deuteronomy 33 in the BOHCV

Deuteronomy 33 in the BOHLNT

Deuteronomy 33 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 33 in the BOICB

Deuteronomy 33 in the BOILNTAP

Deuteronomy 33 in the BOITCV

Deuteronomy 33 in the BOKCV

Deuteronomy 33 in the BOKCV2

Deuteronomy 33 in the BOKHWOG

Deuteronomy 33 in the BOKSSV

Deuteronomy 33 in the BOLCB

Deuteronomy 33 in the BOLCB2

Deuteronomy 33 in the BOMCV

Deuteronomy 33 in the BONAV

Deuteronomy 33 in the BONCB

Deuteronomy 33 in the BONLT

Deuteronomy 33 in the BONUT2

Deuteronomy 33 in the BOPLNT

Deuteronomy 33 in the BOSCB

Deuteronomy 33 in the BOSNC

Deuteronomy 33 in the BOTLNT

Deuteronomy 33 in the BOVCB

Deuteronomy 33 in the BOYCB

Deuteronomy 33 in the BPBB

Deuteronomy 33 in the BPH

Deuteronomy 33 in the BSB

Deuteronomy 33 in the CCB

Deuteronomy 33 in the CUV

Deuteronomy 33 in the CUVS

Deuteronomy 33 in the DBT

Deuteronomy 33 in the DGDNT

Deuteronomy 33 in the DHNT

Deuteronomy 33 in the DNT

Deuteronomy 33 in the ELBE

Deuteronomy 33 in the EMTV

Deuteronomy 33 in the ESV

Deuteronomy 33 in the FBV

Deuteronomy 33 in the FEB

Deuteronomy 33 in the GGMNT

Deuteronomy 33 in the GNT

Deuteronomy 33 in the HARY

Deuteronomy 33 in the HNT

Deuteronomy 33 in the IRVA

Deuteronomy 33 in the IRVB

Deuteronomy 33 in the IRVG

Deuteronomy 33 in the IRVH

Deuteronomy 33 in the IRVK

Deuteronomy 33 in the IRVM

Deuteronomy 33 in the IRVM2

Deuteronomy 33 in the IRVO

Deuteronomy 33 in the IRVP

Deuteronomy 33 in the IRVT

Deuteronomy 33 in the IRVT2

Deuteronomy 33 in the IRVU

Deuteronomy 33 in the ISVN

Deuteronomy 33 in the JSNT

Deuteronomy 33 in the KAPI

Deuteronomy 33 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 33 in the KBV

Deuteronomy 33 in the KJV

Deuteronomy 33 in the KNFD

Deuteronomy 33 in the LBA

Deuteronomy 33 in the LBLA

Deuteronomy 33 in the LNT

Deuteronomy 33 in the LSV

Deuteronomy 33 in the MAAL

Deuteronomy 33 in the MBV

Deuteronomy 33 in the MBV2

Deuteronomy 33 in the MHNT

Deuteronomy 33 in the MKNFD

Deuteronomy 33 in the MNG

Deuteronomy 33 in the MNT

Deuteronomy 33 in the MNT2

Deuteronomy 33 in the MRS1T

Deuteronomy 33 in the NAA

Deuteronomy 33 in the NASB

Deuteronomy 33 in the NBLA

Deuteronomy 33 in the NBS

Deuteronomy 33 in the NBVTP

Deuteronomy 33 in the NET2

Deuteronomy 33 in the NIV11

Deuteronomy 33 in the NNT

Deuteronomy 33 in the NNT2

Deuteronomy 33 in the NNT3

Deuteronomy 33 in the PDDPT

Deuteronomy 33 in the PFNT

Deuteronomy 33 in the RMNT

Deuteronomy 33 in the SBIAS

Deuteronomy 33 in the SBIBS

Deuteronomy 33 in the SBIBS2

Deuteronomy 33 in the SBICS

Deuteronomy 33 in the SBIDS

Deuteronomy 33 in the SBIGS

Deuteronomy 33 in the SBIHS

Deuteronomy 33 in the SBIIS

Deuteronomy 33 in the SBIIS2

Deuteronomy 33 in the SBIIS3

Deuteronomy 33 in the SBIKS

Deuteronomy 33 in the SBIKS2

Deuteronomy 33 in the SBIMS

Deuteronomy 33 in the SBIOS

Deuteronomy 33 in the SBIPS

Deuteronomy 33 in the SBISS

Deuteronomy 33 in the SBITS

Deuteronomy 33 in the SBITS2

Deuteronomy 33 in the SBITS3

Deuteronomy 33 in the SBITS4

Deuteronomy 33 in the SBIUS

Deuteronomy 33 in the SBIVS

Deuteronomy 33 in the SBT

Deuteronomy 33 in the SBT1E

Deuteronomy 33 in the SCHL

Deuteronomy 33 in the SNT

Deuteronomy 33 in the SUSU

Deuteronomy 33 in the SUSU2

Deuteronomy 33 in the SYNO

Deuteronomy 33 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 33 in the TBT1E

Deuteronomy 33 in the TBT1E2

Deuteronomy 33 in the TFTIP

Deuteronomy 33 in the TFTU

Deuteronomy 33 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 33 in the THAI

Deuteronomy 33 in the TNFD

Deuteronomy 33 in the TNT

Deuteronomy 33 in the TNTIK

Deuteronomy 33 in the TNTIL

Deuteronomy 33 in the TNTIN

Deuteronomy 33 in the TNTIP

Deuteronomy 33 in the TNTIZ

Deuteronomy 33 in the TOMA

Deuteronomy 33 in the TTENT

Deuteronomy 33 in the UBG

Deuteronomy 33 in the UGV

Deuteronomy 33 in the UGV2

Deuteronomy 33 in the UGV3

Deuteronomy 33 in the VBL

Deuteronomy 33 in the VDCC

Deuteronomy 33 in the YALU

Deuteronomy 33 in the YAPE

Deuteronomy 33 in the YBVTP

Deuteronomy 33 in the ZBP