Ephesians 5 (BOGWICC)

1 Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu. 2 Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu. 3 Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu. 4 Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika. 5 Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu. 6 Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera. 7 Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere. 8 Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika 9 (pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi). 10 Inu mufufuze chimene chimakondweretsa Ambuye. 11 Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma mʼmalo mwake muzitsutse. 12 Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri. 13 Koma kuwala kumawunikira zinthu, ndipo chilichonse chimaonekera poyera. Choncho chilichonse choonekera poyera chimasandukanso kuwala. 14 Nʼchifukwa chake Malemba akuti,“Dzuka, wamtulo iwe,uka kwa akufa,ndipo Khristu adzakuwalira.” 15 Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru. 16 Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa. 17 Choncho musakhale opusa, koma mudziwe zimene Ambuye akufuna kuti muchite. 18 Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. 19 Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu. 20 Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu. 21 Gonjeranani wina ndi mnzake, kuonetsa kuopa Khristu. 22 Inu akazi, muzigonjera amuna anu, monga mumagonjera kwa Ambuye. 23 Pakuti mwamuna ndi mutu wa mkazi monga momwe Khristu ali mutu wa mpingo, thupi lake, limene Iyeyo ndi Mpulumutsi wake. 24 Tsono monga mpingo umagonjera Khristu, momwemonso akazi akuyenera kugonjera amuna awo mu zonse. 25 Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo 26 kuti awupatule ukhale oyera, atawuyeretsa powusambitsa ndi madzi omwe ndi mawu ake. 27 Anachita zimenezi kuti awupereke mpingowo kwa Iye mwini, mpingo wowala ndi waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapena chilema chilichonse, koma oyera ndi wangwiro. 28 Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha. 29 Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake 30 pakuti ndife ziwalo za thupi lake. 31 “Pa chifukwa ichi, mwamuna adzasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.” 32 Ichi ndi chinsinsi chozama, koma ine ndikunena za Khristu ndi mpingo. 33 Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake.

In Other Versions

Ephesians 5 in the ANGEFD

Ephesians 5 in the ANTPNG2D

Ephesians 5 in the AS21

Ephesians 5 in the BAGH

Ephesians 5 in the BBPNG

Ephesians 5 in the BBT1E

Ephesians 5 in the BDS

Ephesians 5 in the BEV

Ephesians 5 in the BHAD

Ephesians 5 in the BIB

Ephesians 5 in the BLPT

Ephesians 5 in the BNT

Ephesians 5 in the BNTABOOT

Ephesians 5 in the BNTLV

Ephesians 5 in the BOATCB

Ephesians 5 in the BOATCB2

Ephesians 5 in the BOBCV

Ephesians 5 in the BOCNT

Ephesians 5 in the BOECS

Ephesians 5 in the BOHCB

Ephesians 5 in the BOHCV

Ephesians 5 in the BOHLNT

Ephesians 5 in the BOHNTLTAL

Ephesians 5 in the BOICB

Ephesians 5 in the BOILNTAP

Ephesians 5 in the BOITCV

Ephesians 5 in the BOKCV

Ephesians 5 in the BOKCV2

Ephesians 5 in the BOKHWOG

Ephesians 5 in the BOKSSV

Ephesians 5 in the BOLCB

Ephesians 5 in the BOLCB2

Ephesians 5 in the BOMCV

Ephesians 5 in the BONAV

Ephesians 5 in the BONCB

Ephesians 5 in the BONLT

Ephesians 5 in the BONUT2

Ephesians 5 in the BOPLNT

Ephesians 5 in the BOSCB

Ephesians 5 in the BOSNC

Ephesians 5 in the BOTLNT

Ephesians 5 in the BOVCB

Ephesians 5 in the BOYCB

Ephesians 5 in the BPBB

Ephesians 5 in the BPH

Ephesians 5 in the BSB

Ephesians 5 in the CCB

Ephesians 5 in the CUV

Ephesians 5 in the CUVS

Ephesians 5 in the DBT

Ephesians 5 in the DGDNT

Ephesians 5 in the DHNT

Ephesians 5 in the DNT

Ephesians 5 in the ELBE

Ephesians 5 in the EMTV

Ephesians 5 in the ESV

Ephesians 5 in the FBV

Ephesians 5 in the FEB

Ephesians 5 in the GGMNT

Ephesians 5 in the GNT

Ephesians 5 in the HARY

Ephesians 5 in the HNT

Ephesians 5 in the IRVA

Ephesians 5 in the IRVB

Ephesians 5 in the IRVG

Ephesians 5 in the IRVH

Ephesians 5 in the IRVK

Ephesians 5 in the IRVM

Ephesians 5 in the IRVM2

Ephesians 5 in the IRVO

Ephesians 5 in the IRVP

Ephesians 5 in the IRVT

Ephesians 5 in the IRVT2

Ephesians 5 in the IRVU

Ephesians 5 in the ISVN

Ephesians 5 in the JSNT

Ephesians 5 in the KAPI

Ephesians 5 in the KBT1ETNIK

Ephesians 5 in the KBV

Ephesians 5 in the KJV

Ephesians 5 in the KNFD

Ephesians 5 in the LBA

Ephesians 5 in the LBLA

Ephesians 5 in the LNT

Ephesians 5 in the LSV

Ephesians 5 in the MAAL

Ephesians 5 in the MBV

Ephesians 5 in the MBV2

Ephesians 5 in the MHNT

Ephesians 5 in the MKNFD

Ephesians 5 in the MNG

Ephesians 5 in the MNT

Ephesians 5 in the MNT2

Ephesians 5 in the MRS1T

Ephesians 5 in the NAA

Ephesians 5 in the NASB

Ephesians 5 in the NBLA

Ephesians 5 in the NBS

Ephesians 5 in the NBVTP

Ephesians 5 in the NET2

Ephesians 5 in the NIV11

Ephesians 5 in the NNT

Ephesians 5 in the NNT2

Ephesians 5 in the NNT3

Ephesians 5 in the PDDPT

Ephesians 5 in the PFNT

Ephesians 5 in the RMNT

Ephesians 5 in the SBIAS

Ephesians 5 in the SBIBS

Ephesians 5 in the SBIBS2

Ephesians 5 in the SBICS

Ephesians 5 in the SBIDS

Ephesians 5 in the SBIGS

Ephesians 5 in the SBIHS

Ephesians 5 in the SBIIS

Ephesians 5 in the SBIIS2

Ephesians 5 in the SBIIS3

Ephesians 5 in the SBIKS

Ephesians 5 in the SBIKS2

Ephesians 5 in the SBIMS

Ephesians 5 in the SBIOS

Ephesians 5 in the SBIPS

Ephesians 5 in the SBISS

Ephesians 5 in the SBITS

Ephesians 5 in the SBITS2

Ephesians 5 in the SBITS3

Ephesians 5 in the SBITS4

Ephesians 5 in the SBIUS

Ephesians 5 in the SBIVS

Ephesians 5 in the SBT

Ephesians 5 in the SBT1E

Ephesians 5 in the SCHL

Ephesians 5 in the SNT

Ephesians 5 in the SUSU

Ephesians 5 in the SUSU2

Ephesians 5 in the SYNO

Ephesians 5 in the TBIAOTANT

Ephesians 5 in the TBT1E

Ephesians 5 in the TBT1E2

Ephesians 5 in the TFTIP

Ephesians 5 in the TFTU

Ephesians 5 in the TGNTATF3T

Ephesians 5 in the THAI

Ephesians 5 in the TNFD

Ephesians 5 in the TNT

Ephesians 5 in the TNTIK

Ephesians 5 in the TNTIL

Ephesians 5 in the TNTIN

Ephesians 5 in the TNTIP

Ephesians 5 in the TNTIZ

Ephesians 5 in the TOMA

Ephesians 5 in the TTENT

Ephesians 5 in the UBG

Ephesians 5 in the UGV

Ephesians 5 in the UGV2

Ephesians 5 in the UGV3

Ephesians 5 in the VBL

Ephesians 5 in the VDCC

Ephesians 5 in the YALU

Ephesians 5 in the YAPE

Ephesians 5 in the YBVTP

Ephesians 5 in the ZBP