Isaiah 60 (BOGWICC)
1 “Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika,ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira. 2 Taona, mdima waphimba dziko lapansindipo mdima wandiweyani wagwa pa anthu a mitundu ina,koma Yehova adzakuwalira iwe,ndipo ulemerero wake udzaoneka pa iwe. 3 Mitundu ya anthu idzatsata kuwunika kwakondipo mafumu adzalondola kunyezimira kwa mʼbandakucha wako. 4 “Tukula maso ako, yangʼanayangʼana ndipo ona zimene zikuchitika.Onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe;ana ako a amuna akubwera kuchokera kutalindipo ana ako aakazi anyamulidwa mʼmanja. 5 Ukadzaona zimenezi udzasangalala kwambiri,mtima wako udzalumpha ndi kudzaza ndi chimwemwe;chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwechuma cha mitundu ya anthu chidzabwera kwa iwe. 6 Gulu la ngamira lidzaphimba dziko lako,ngamira zingʼonozingʼono zidzachokera ku Midiyani ndi ku Efai.Ndipo onse a ku Seba adzabweraatanyamula golide ndi lubaniuku akutamanda Yehova. 7 Ziweto zonse za ku Kedara adzazisonkhanitsa kwa inu,nkhosa zazimuna za ku Nabayoti zidzakutumikirani;zidzalandiridwa monga chopereka pa guwa langa la nsembe,ndipo ndidzakongoletsa Nyumba yanga. 8 “Kodi ndi zayani izo zikuwuluka ngati mitambo,ngati kapena nkhunda zobwerera ku zisa zawo? 9 Ndithu, izi ndi sitima za pa madzi zochokera ku mayiko akutali;patsogolo pali sitima zapamadzi za ku Tarisisi,zikubweretsa ana ako ochokera kutali,pamodzi ndi siliva wawo ndi golide wawo,kudzalemekeza Yehova Mulungu wako,Woyerayo wa Israeli,pakuti Iye wakuvekani inu ulemerero. 10 “Alendo adzamanganso malinga ako,ndipo mafumu awo adzakutumikira.Ngakhale ndinakukantha ndili wokwiya,koma tsopano ndidzakukomera mtima ndikukuchitira chifundo. 11 Zipata zako zidzakhala zotsekula nthawi zonse,sadzazitseka nthawi zonse, usana ndi usiku,kotero anthu adzabwera kwa iwe ndi chuma chawo,akuyenda pa mdipiti mafumu awo ali patsogolo. 12 Pakuti mtundu wa anthu ndi mafumu amene sakutumikira iwe;adzawonongeka kotheratu. 13 “Adzabwera nayo kwa iwe mitengo ya payini,mkuyu ndi naphini imene ili mʼnkhalango ya Lebanonikuti adzakongoletsere malo a nyumba yanga yopatulika;ndipo ndidzalemekeza malo amene Ine ndimapondapo. 14 Ana aja amene anakuzunzani adzabwera ndipo adzakugwadirani;onse amene anakunyozani adzagwada pansi pa mapazi anu.Ndipo adzakutchani kuti Mzinda wa Yehova;Ziyoni mzinda wa Woyerayo wa Israeli. 15 “Ngakhale anthu anakusiya nadana nawe,koma Ine ndidzakukuza mpaka muyaya,ndipo udzakhala malo a chimwemwecha anthu amibado yonse. 16 Udzamwa mkaka wa mitundu ya anthundi kuleredwa pa maere aufumu,motero udzadziwa kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wako,Momboli wako ndiye Wamphamvu wa Yakobo. 17 Ndidzakupatsa golide mʼmalo mwa mkuwa,ndi siliva mʼmalo mwa chitsulo.Ndidzakupatsa mkuwa mʼmalo mwa thabwandi chitsulo mʼmalo mwa miyala.Olamulira ako adzakhala a mtendere.Ndidzasandutsa okulamulira kuti akhale achilungamo. 18 Ziwawa sizidzamvekanso mʼdziko lako,bwinja kapena chiwonongeko sizidzapezeka mʼdziko lako,ndidzakhala malinga ako okutetezandipo udzanditamanda. 19 Sipadzakhala dzuwa kuti likuwunikire,kapena mwezi kuti uwunikire usiku,pakuti Yehova ndiye adzakhale kuwunika kwako kwa muyaya,ndipo Mulungu wako adzakhala ulemerero wako. 20 Dzuwa lako silidzalowanso,ndipo mwezi wako sudzazimiriranso;Yehova adzakhala kuwunika kwako kwamuyaya,ndipo masiku a mavuto ako adzatha. 21 Ndipo anthu ako onse adzakhala olungamandipo dzikolo lidzakhala lawo mpaka muyaya.Iwo ndi mphukira imene Ine ndayidzala,ntchito ya manja anga,kuti aonetse ulemerero wanga. 22 Kabanja kakangʼono kadzasanduka fuko,kafuko kakangʼono kudzasanduka mtundu wamphamvu.Ine ndine Yehova,nthawi yake ikafika ndidzazichita zimenezi mofulumira.”
In Other Versions
Isaiah 60 in the ANGEFD
Isaiah 60 in the ANTPNG2D
Isaiah 60 in the AS21
Isaiah 60 in the BAGH
Isaiah 60 in the BBPNG
Isaiah 60 in the BBT1E
Isaiah 60 in the BDS
Isaiah 60 in the BEV
Isaiah 60 in the BHAD
Isaiah 60 in the BIB
Isaiah 60 in the BLPT
Isaiah 60 in the BNT
Isaiah 60 in the BNTABOOT
Isaiah 60 in the BNTLV
Isaiah 60 in the BOATCB
Isaiah 60 in the BOATCB2
Isaiah 60 in the BOBCV
Isaiah 60 in the BOCNT
Isaiah 60 in the BOECS
Isaiah 60 in the BOHCB
Isaiah 60 in the BOHCV
Isaiah 60 in the BOHLNT
Isaiah 60 in the BOHNTLTAL
Isaiah 60 in the BOICB
Isaiah 60 in the BOILNTAP
Isaiah 60 in the BOITCV
Isaiah 60 in the BOKCV
Isaiah 60 in the BOKCV2
Isaiah 60 in the BOKHWOG
Isaiah 60 in the BOKSSV
Isaiah 60 in the BOLCB
Isaiah 60 in the BOLCB2
Isaiah 60 in the BOMCV
Isaiah 60 in the BONAV
Isaiah 60 in the BONCB
Isaiah 60 in the BONLT
Isaiah 60 in the BONUT2
Isaiah 60 in the BOPLNT
Isaiah 60 in the BOSCB
Isaiah 60 in the BOSNC
Isaiah 60 in the BOTLNT
Isaiah 60 in the BOVCB
Isaiah 60 in the BOYCB
Isaiah 60 in the BPBB
Isaiah 60 in the BPH
Isaiah 60 in the BSB
Isaiah 60 in the CCB
Isaiah 60 in the CUV
Isaiah 60 in the CUVS
Isaiah 60 in the DBT
Isaiah 60 in the DGDNT
Isaiah 60 in the DHNT
Isaiah 60 in the DNT
Isaiah 60 in the ELBE
Isaiah 60 in the EMTV
Isaiah 60 in the ESV
Isaiah 60 in the FBV
Isaiah 60 in the FEB
Isaiah 60 in the GGMNT
Isaiah 60 in the GNT
Isaiah 60 in the HARY
Isaiah 60 in the HNT
Isaiah 60 in the IRVA
Isaiah 60 in the IRVB
Isaiah 60 in the IRVG
Isaiah 60 in the IRVH
Isaiah 60 in the IRVK
Isaiah 60 in the IRVM
Isaiah 60 in the IRVM2
Isaiah 60 in the IRVO
Isaiah 60 in the IRVP
Isaiah 60 in the IRVT
Isaiah 60 in the IRVT2
Isaiah 60 in the IRVU
Isaiah 60 in the ISVN
Isaiah 60 in the JSNT
Isaiah 60 in the KAPI
Isaiah 60 in the KBT1ETNIK
Isaiah 60 in the KBV
Isaiah 60 in the KJV
Isaiah 60 in the KNFD
Isaiah 60 in the LBA
Isaiah 60 in the LBLA
Isaiah 60 in the LNT
Isaiah 60 in the LSV
Isaiah 60 in the MAAL
Isaiah 60 in the MBV
Isaiah 60 in the MBV2
Isaiah 60 in the MHNT
Isaiah 60 in the MKNFD
Isaiah 60 in the MNG
Isaiah 60 in the MNT
Isaiah 60 in the MNT2
Isaiah 60 in the MRS1T
Isaiah 60 in the NAA
Isaiah 60 in the NASB
Isaiah 60 in the NBLA
Isaiah 60 in the NBS
Isaiah 60 in the NBVTP
Isaiah 60 in the NET2
Isaiah 60 in the NIV11
Isaiah 60 in the NNT
Isaiah 60 in the NNT2
Isaiah 60 in the NNT3
Isaiah 60 in the PDDPT
Isaiah 60 in the PFNT
Isaiah 60 in the RMNT
Isaiah 60 in the SBIAS
Isaiah 60 in the SBIBS
Isaiah 60 in the SBIBS2
Isaiah 60 in the SBICS
Isaiah 60 in the SBIDS
Isaiah 60 in the SBIGS
Isaiah 60 in the SBIHS
Isaiah 60 in the SBIIS
Isaiah 60 in the SBIIS2
Isaiah 60 in the SBIIS3
Isaiah 60 in the SBIKS
Isaiah 60 in the SBIKS2
Isaiah 60 in the SBIMS
Isaiah 60 in the SBIOS
Isaiah 60 in the SBIPS
Isaiah 60 in the SBISS
Isaiah 60 in the SBITS
Isaiah 60 in the SBITS2
Isaiah 60 in the SBITS3
Isaiah 60 in the SBITS4
Isaiah 60 in the SBIUS
Isaiah 60 in the SBIVS
Isaiah 60 in the SBT
Isaiah 60 in the SBT1E
Isaiah 60 in the SCHL
Isaiah 60 in the SNT
Isaiah 60 in the SUSU
Isaiah 60 in the SUSU2
Isaiah 60 in the SYNO
Isaiah 60 in the TBIAOTANT
Isaiah 60 in the TBT1E
Isaiah 60 in the TBT1E2
Isaiah 60 in the TFTIP
Isaiah 60 in the TFTU
Isaiah 60 in the TGNTATF3T
Isaiah 60 in the THAI
Isaiah 60 in the TNFD
Isaiah 60 in the TNT
Isaiah 60 in the TNTIK
Isaiah 60 in the TNTIL
Isaiah 60 in the TNTIN
Isaiah 60 in the TNTIP
Isaiah 60 in the TNTIZ
Isaiah 60 in the TOMA
Isaiah 60 in the TTENT
Isaiah 60 in the UBG
Isaiah 60 in the UGV
Isaiah 60 in the UGV2
Isaiah 60 in the UGV3
Isaiah 60 in the VBL
Isaiah 60 in the VDCC
Isaiah 60 in the YALU
Isaiah 60 in the YAPE
Isaiah 60 in the YBVTP
Isaiah 60 in the ZBP