Job 33 (BOGWICC)

1 “Koma tsopano, inu abambo Yobu chonde mverani mawu anga;mutcherere khutu zonse zimene ndinene. 2 Tsopano ndiyamba kuyankhula;mawu anga ali pa msonga ya lilime langa. 3 Mawu anga akuchokera mu mtima wolungama;pakamwa panga pakuyankhula zoonadi zimene ndikuzidziwa. 4 Mzimu wa Mulungu wandiwumba,mpweya wa Wamphamvuzonse umandipatsa moyo. 5 Mundiyankhe ngati mungathe;konzekani tsopano kuti munditsutse. 6 Ine ndili monga inu pamaso pa Mulungu;nanenso ndinachokera ku dothi. 7 Musachite mantha ndipo musandiope ayi,Ine sindikupanikizani kwambiri ayi. 8 “Koma inu mwayankhula ine ndikumva,ndamva mawu anuwo onena kuti, 9 ‘Ndine wolungama mtima ndi wopanda tchimo;ndine woyera mtima ndipo ndilibe cholakwa. 10 Komatu Mulungu wapeza zifukwa zoti anditsutsire nazo;Iye akundiyesa ngati mdani wake. 11 Iyeyo wamanga mapazi anga mʼzigologolo,akulonda mayendedwe anga onse.’ 12 “Koma ine ndi kuti kwa inu, inuyo simukukhoza pa zimenezi,pakuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu. 13 Chifukwa chiyani mukudandaula kwa Iyekuti sayankha mawu ena aliwonse a munthu? 14 Pajatu Mulungu amayankhula mwa njira zosiyanasiyana,ngakhale munthu sazindikira zimenezi. 15 Mʼmaloto, mʼmasomphenya usiku,pamene anthu ali mʼtulo tofa natopamene akungosinza chabe pa bedi, 16 amawanongʼoneza mʼmakutundi kuwaopseza ndi machenjezo ake, 17 kumuchotsa munthu ku zoyipa,ndi kuthetseratu kunyada kwake, 18 kumulanditsa munthu ku manda,kuti moyo wake usawonongeke ndi lupanga. 19 “Mwina Mulungu amalanga munthu ndi matenda ndi ululu ali pa bedi pake,nthawiyo thupi lake lonse limangophwanya, 20 kuti asakhalenso ndi chilakolako cha chakudya,ndipo amanyansidwa ndi chakudya chabwino chomwe. 21 Thupi lake limawondandipo mafupa ake, omwe anali obisika, tsopano amaonekera poyera. 22 Munthuyo amayandikira ku manda,moyo wake umayandikira kwa amene amabweretsa imfa. 23 “Koma patakhala mngelo ngati mthandizi,mmodzi mwa ambirimbiri oterewa,adzafotokoza zimene zili zoyenera, 24 kudzamukomera mtima ndi kunena kuti,‘Mupulumutseni kuti asapite ku manda;ine ndapeza cholowa mʼmalo mwa moyo wake,’ 25 pamenepo thupi lake lidzasanduka lasee ngati la mwana;ndipo adzabwezeretsedwanso kukhala ngati mʼmasiku a unyamata wake. 26 Akapemphera kwa Mulungu, iyeyo adzalandiridwa.Mulungu adzamulandira mwa chimwemwendipo adzamubwezeretsa pamalo ake oyamba. 27 Ndipo adzabwera kwa anzake ndi kunena kuti,‘Ndinachimwa ndipo sindinachite zolungama,koma sindinalangidwe koyenerana ndi kuchimwa kwanga. 28 Iye anapulumutsa moyo wanga kuti usapite ku manda,ndipo ndidzakhala ndi moyo ndi kuonanso kuwala kwa dzuwa.’ 29 “Mulungu amachita zonsezi kwa munthukawirikawiri, 30 kupulumutsa moyo wa munthuyo ku manda,kuti athe kuonanso kuwala kwa moyo. 31 “Abambo Yobu, tcherani khutu ndipo mundimvere;khalani chete kuti ndiyankhule. 32 Ngati muli nʼchoti munene, ndiyankheni;yankhulani, pakuti ine ndikufuna mupezeke wolungama. 33 Koma ngati sichoncho, mundimvere;khalani chete ndipo ine ndidzakuphunzitsani nzeru.”

In Other Versions

Job 33 in the ANGEFD

Job 33 in the ANTPNG2D

Job 33 in the AS21

Job 33 in the BAGH

Job 33 in the BBPNG

Job 33 in the BBT1E

Job 33 in the BDS

Job 33 in the BEV

Job 33 in the BHAD

Job 33 in the BIB

Job 33 in the BLPT

Job 33 in the BNT

Job 33 in the BNTABOOT

Job 33 in the BNTLV

Job 33 in the BOATCB

Job 33 in the BOATCB2

Job 33 in the BOBCV

Job 33 in the BOCNT

Job 33 in the BOECS

Job 33 in the BOHCB

Job 33 in the BOHCV

Job 33 in the BOHLNT

Job 33 in the BOHNTLTAL

Job 33 in the BOICB

Job 33 in the BOILNTAP

Job 33 in the BOITCV

Job 33 in the BOKCV

Job 33 in the BOKCV2

Job 33 in the BOKHWOG

Job 33 in the BOKSSV

Job 33 in the BOLCB

Job 33 in the BOLCB2

Job 33 in the BOMCV

Job 33 in the BONAV

Job 33 in the BONCB

Job 33 in the BONLT

Job 33 in the BONUT2

Job 33 in the BOPLNT

Job 33 in the BOSCB

Job 33 in the BOSNC

Job 33 in the BOTLNT

Job 33 in the BOVCB

Job 33 in the BOYCB

Job 33 in the BPBB

Job 33 in the BPH

Job 33 in the BSB

Job 33 in the CCB

Job 33 in the CUV

Job 33 in the CUVS

Job 33 in the DBT

Job 33 in the DGDNT

Job 33 in the DHNT

Job 33 in the DNT

Job 33 in the ELBE

Job 33 in the EMTV

Job 33 in the ESV

Job 33 in the FBV

Job 33 in the FEB

Job 33 in the GGMNT

Job 33 in the GNT

Job 33 in the HARY

Job 33 in the HNT

Job 33 in the IRVA

Job 33 in the IRVB

Job 33 in the IRVG

Job 33 in the IRVH

Job 33 in the IRVK

Job 33 in the IRVM

Job 33 in the IRVM2

Job 33 in the IRVO

Job 33 in the IRVP

Job 33 in the IRVT

Job 33 in the IRVT2

Job 33 in the IRVU

Job 33 in the ISVN

Job 33 in the JSNT

Job 33 in the KAPI

Job 33 in the KBT1ETNIK

Job 33 in the KBV

Job 33 in the KJV

Job 33 in the KNFD

Job 33 in the LBA

Job 33 in the LBLA

Job 33 in the LNT

Job 33 in the LSV

Job 33 in the MAAL

Job 33 in the MBV

Job 33 in the MBV2

Job 33 in the MHNT

Job 33 in the MKNFD

Job 33 in the MNG

Job 33 in the MNT

Job 33 in the MNT2

Job 33 in the MRS1T

Job 33 in the NAA

Job 33 in the NASB

Job 33 in the NBLA

Job 33 in the NBS

Job 33 in the NBVTP

Job 33 in the NET2

Job 33 in the NIV11

Job 33 in the NNT

Job 33 in the NNT2

Job 33 in the NNT3

Job 33 in the PDDPT

Job 33 in the PFNT

Job 33 in the RMNT

Job 33 in the SBIAS

Job 33 in the SBIBS

Job 33 in the SBIBS2

Job 33 in the SBICS

Job 33 in the SBIDS

Job 33 in the SBIGS

Job 33 in the SBIHS

Job 33 in the SBIIS

Job 33 in the SBIIS2

Job 33 in the SBIIS3

Job 33 in the SBIKS

Job 33 in the SBIKS2

Job 33 in the SBIMS

Job 33 in the SBIOS

Job 33 in the SBIPS

Job 33 in the SBISS

Job 33 in the SBITS

Job 33 in the SBITS2

Job 33 in the SBITS3

Job 33 in the SBITS4

Job 33 in the SBIUS

Job 33 in the SBIVS

Job 33 in the SBT

Job 33 in the SBT1E

Job 33 in the SCHL

Job 33 in the SNT

Job 33 in the SUSU

Job 33 in the SUSU2

Job 33 in the SYNO

Job 33 in the TBIAOTANT

Job 33 in the TBT1E

Job 33 in the TBT1E2

Job 33 in the TFTIP

Job 33 in the TFTU

Job 33 in the TGNTATF3T

Job 33 in the THAI

Job 33 in the TNFD

Job 33 in the TNT

Job 33 in the TNTIK

Job 33 in the TNTIL

Job 33 in the TNTIN

Job 33 in the TNTIP

Job 33 in the TNTIZ

Job 33 in the TOMA

Job 33 in the TTENT

Job 33 in the UBG

Job 33 in the UGV

Job 33 in the UGV2

Job 33 in the UGV3

Job 33 in the VBL

Job 33 in the VDCC

Job 33 in the YALU

Job 33 in the YAPE

Job 33 in the YBVTP

Job 33 in the ZBP