Lamentations 1 (BOGWICC)
1 Haa! Mzinda uja wasiyidwa wokhawokha,umene kale unali wodzaza ndi anthu!Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu!Tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye.Kale unali mfumukazi ya onse pa dziko lapansi,tsopano wasanduka kapolo. 2 Ukulira mowawidwa mtima usiku wonse,misozi ili pa masaya pake.Mwa abwenzi ake onse,palibe ndi mmodzi yemwe womutonthoza.Abwenzi ake onse amuchitira chiwembu;onse akhala adani ake. 3 Yuda watengedwa ku ukapolo,kukazunzika ndi kukagwira ntchito yolemetsa.Iye akukhala pakati pa anthu a mitundu ina;ndipo alibe malo opumulira.Onse omuthamangitsa iye amupitirira,ndipo alibe kwina kothawira. 4 Misewu yopita ku Ziyoni ikulira,chifukwa palibe ndi mmodzi yemwe akubwera ku maphwando ake.Zipata zake zonse zili pululu,ansembe akubuwula.Anamwali ake akulira,ndipo ali mʼmasautso woopsa. 5 Adani ake asanduka mabwana ake;odana naye akupeza bwino.Yehova wamubweretsera mavutochifukwa cha machimo ake ambiri.Ana ake atengedwa ukapolopamaso pa mdani. 6 Ulemerero wonse wa mwana wamkazi wa Ziyoniwachokeratu.Akalonga ake ali ngati mbawalazosowa msipu;alibe mphamvu zothawiraowathamangitsa. 7 Pa masiku a masautso ndi kuzunzika kwake,Yerusalemu amakumbukira chuma chonsechimene mʼmasiku amakedzana chinali chake.Anthu ake atagwidwa ndi adani ake,panalibe aliyense womuthandiza.Adani ake ankamuyangʼanandi kumuseka chifukwa cha kuwonongeka kwake. 8 Yerusalemu wachimwa kwambirindipo potero wakhala wodetsedwa.Onse amene ankamulemekeza pano akumunyoza,chifukwa aona umaliseche wake.Iye mwini akubuwulandipo akubisa nkhope yake. 9 Uve wake umaonekera pa zovala zake;iye sanaganizire za tsogolo lake.Nʼchifukwa chake kugwa kwake kunali kwakukulu;ndipo analibe womutonthoza.“Inu Yehova, taonani masautso anga,pakuti mdani wapambana.” 10 Adani amulandachuma chake chonse;iye anaona mitundu ya anthu achikunja ikulowa mʼmalo ake opatulika,amene Inu Mulungu munawaletsakulowa mu msonkhano wanu. 11 Anthu ake onse akubuwulapamene akufunafuna chakudya;asinthanitsa chuma chawo ndi chakudyakuti akhale ndi moyo.“Inu Yehova, taonani ndipo ganizirani,chifukwa ine ndanyozeka.” 12 “Kodi zimenezi mukuziyesa zachabe, inu nonse mukudutsa?Yangʼanani ndipo muone.Kodi pali mavuto ofanana ndiamene andigwerawa,amene Ambuye anandibweretserapa tsiku la ukali wake? 13 “Anatumiza moto kuchokera kumwamba,unalowa mpaka mʼmafupa anga.Anayala ukonde kuti ukole mapazi angandipo anandibweza.Anandisiya wopanda chilichonse,wolefuka tsiku lonse. 14 “Wazindikira machimo anga onsendipo ndi manja ake anawaluka pamodzi.Machimowa afika pakhosi panga,ndipo Ambuye wandithetsa mphamvu.Iye wandiperekakwa anthu amene sindingalimbane nawo. 15 “Ambuye wakanaanthu anga onse amphamvu omwe ankakhala nane:wasonkhanitsa gulu lankhondo kuti lilimbane nane,kuti litekedze anyamata anga;mʼmalo ofinyira mphesa Ambuye waponderezaanamwali a Yuda. 16 “Chifukwa cha zimenezi ndikulirandipo maso anga adzaza ndi misozi.Palibe aliyense pafupi woti anditonthoze,palibe aliyense wondilimbitsa mtima.Ana anga ali okhaokhachifukwa mdani watigonjetsa. 17 “Ziyoni wakweza manja ake,koma palibe aliyense womutonthoza.Yehova walamula kuti abale akea Yakobo akhale adani ake;Yerusalemu wasandukachinthu chodetsedwa pakati pawo. 18 “Yehova ndi wolungama,koma ndine ndinawukira malamulo ake.Imvani inu anthu a mitundu yonse;onani masautso anga.Anyamata ndi anamwali angaagwidwa ukapolo. 19 “Ndinayitana abwenzi angakoma anandinyenga.Ansembe ndi akuluakulu angaanafa mu mzindapamene ankafunafuna chakudyakuti akhale ndi moyo. 20 “Inu Yehova, onani mmene ine ndavutikira!Ndikuzunzika mʼkati mwanga,ndipo mu mtima mwanga ndasautsidwachifukwa ndakhala osamvera.Mʼmisewu anthu akuphedwa,ndipo ku mudzi kuli imfa yokhayokha. 21 “Anthu amva kubuwula kwanga,koma palibe wonditonthoza.Adani anga onse amva masautso anga;iwo akusangalala pa zimene Inu mwachita.Lifikitseni tsiku limene munalonjeza lijakuti iwonso adzakhale ngati ine. 22 “Lolani kuti ntchito zawo zoyipa zifike pamaso panu;muwalangengati mmene mwandilangira inechifukwa cha machimo anga onse.Ndikubuwula kwambirindipo mtima wanga walefuka.”
In Other Versions
Lamentations 1 in the ANTPNG2D
Lamentations 1 in the BNTABOOT
Lamentations 1 in the BOHNTLTAL
Lamentations 1 in the BOILNTAP
Lamentations 1 in the KBT1ETNIK
Lamentations 1 in the TBIAOTANT