Psalms 107 (BOGWICC)

1 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;pakuti chikondi chake ndi chosatha. 2 Owomboledwa a Yehova anene zimeneziamene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani, 3 iwo amene anawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko,kuchokera kumadzulo ndi kummawa, kuchokera kumpoto ndi kummwera. 4 Ena anayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu,osapeza njira yopitira ku mzinda kumene akanakakhazikikako. 5 Iwo anamva njala ndi ludzu,ndipo miyoyo yawo inafowokeratu. 6 Pamenepo analirira Yehova mʼmavuto awondipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo. 7 Iye anawatsogolera mʼnjira yowongokakupita ku mzinda umene anakakhazikikako. 8 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosathandi chifukwa cha machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse, 9 pakuti Iye wapha ludzu la munthu womva ludzundipo wakhutitsa wanjala ndi zinthu zabwino. 10 Ena anakhala mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu,amʼndende ovutika mʼmaunyolo achitsulo, 11 pakuti iwowo anawukira mawu a Mulungundi kunyoza uphungu wa Wammwambamwamba. 12 Kotero Iye anawapereka kuti agwire ntchito yakalavulagaga;anagwa pansi ndipo panalibe woti awathandize. 13 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awondipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo. 14 Yehova anawatulutsa mu mdima ndi mʼchisoni chachikulundipo anadula maunyolo awo. 15 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosathandi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse, 16 pakuti Iye amathyola zipata zamkuwandi kudula pakati mipiringidzo yachitsulo. 17 Ena anakhala zitsiru chifukwa cha njira zawo zowukira,ndipo anamva zowawa chifukwa cha mphulupulu zawo. 18 Iwo ananyansidwa ndi chakudya chilichonsendipo anafika pafupi ndi zipata za imfa. 19 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awondipo Iye anawapulumutsa ku masautso awowo. 20 Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa;anawalanditsa ku manda. 21 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosathandi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu. 22 Apereke nsembe yachiyamikondi kufotokoza za ntchito zake ndi nyimbo zachimwemwe. 23 Ena anayenda pa nyanja mʼsitima zapamadzi;Iwo anali anthu amalonda pa nyanja yayikulu. 24 Anaona ntchito za Yehova,machitidwe ake odabwitsa mʼnyanja yakuya. 25 Pakuti Iye anayankhula ndi kuwutsa mphepo yamkunthoimene inabweretsa mafunde ataliatali. 26 Sitima za pamadzizo zinatukulidwa mmwamba ndi kutsikira pansi pakuya;pamene amawonongeka, kulimba mtima kwawo kunasungunuka. 27 Anachita chizungulire ndi kudzandira ngati anthu oledzera;anali pa mapeto a moyo wawo. 28 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awondipo Iyeyo anawapulumutsa ku masautso awo. 29 Yehova analetsa namondwe,mafunde a mʼnyanja anatontholetsedwa. 30 Anali osangalala pamene kunakhala bata,ndipo Iye anawatsogolera ku dooko limene amalifuna. 31 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosathandi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu. 32 Akuze Iye mu msonkhano wa anthundi kumutamanda pabwalo la akuluakulu. 33 Iye anasandutsa mitsinje kukhala chipululu,akasupe otuluka madzi kukhala nthaka yowuma, 34 ndiponso nthaka yachonde kukhala nthaka yamchere,chifukwa cha kuyipa kwa amene amakhala kumeneko. 35 Anasandutsa chipululu kukhala mayiwe a madzindi nthaka yowuma kukhala akasupe a madzi oyenda; 36 kumeneko Iye anabweretsa anthu anjala kuti azikhalako,ndipo iwo anamanga mzinda woti akhazikikeko. 37 Anafesa mbewu mʼminda ndi kudzala mipesandipo anakolola zipatso zochuluka; 38 Yehova anawadalitsa, ndipo chiwerengero chawo chinachuluka kwambiri,ndipo Iye sanalole kuti ziweto zawo zithe. 39 Kenaka chiwerengero chawo chinachepa ndipo iwo anatsitsidwachifukwa cha mazunzo, mavuto ndi chisoni; 40 Iye amene amakhuthulira mʼnyozo pa olemekezekaanawachititsa kuyendayenda mʼmalo owumawo wopanda njira. 41 Koma Iyeyo anakweza anthu osowa kuchoka ku masautso awongati magulu a nkhosa. 42 Anthu olungama mtima amaona ndi kusangalala,koma anthu onse oyipa amatseka pakamwa pawo. 43 Aliyense wanzeru asamalitse zinthu zimenezindi kuganizira za chikondi chachikulu cha Yehova.

In Other Versions

Psalms 107 in the ANGEFD

Psalms 107 in the ANTPNG2D

Psalms 107 in the AS21

Psalms 107 in the BAGH

Psalms 107 in the BBPNG

Psalms 107 in the BBT1E

Psalms 107 in the BDS

Psalms 107 in the BEV

Psalms 107 in the BHAD

Psalms 107 in the BIB

Psalms 107 in the BLPT

Psalms 107 in the BNT

Psalms 107 in the BNTABOOT

Psalms 107 in the BNTLV

Psalms 107 in the BOATCB

Psalms 107 in the BOATCB2

Psalms 107 in the BOBCV

Psalms 107 in the BOCNT

Psalms 107 in the BOECS

Psalms 107 in the BOHCB

Psalms 107 in the BOHCV

Psalms 107 in the BOHLNT

Psalms 107 in the BOHNTLTAL

Psalms 107 in the BOICB

Psalms 107 in the BOILNTAP

Psalms 107 in the BOITCV

Psalms 107 in the BOKCV

Psalms 107 in the BOKCV2

Psalms 107 in the BOKHWOG

Psalms 107 in the BOKSSV

Psalms 107 in the BOLCB

Psalms 107 in the BOLCB2

Psalms 107 in the BOMCV

Psalms 107 in the BONAV

Psalms 107 in the BONCB

Psalms 107 in the BONLT

Psalms 107 in the BONUT2

Psalms 107 in the BOPLNT

Psalms 107 in the BOSCB

Psalms 107 in the BOSNC

Psalms 107 in the BOTLNT

Psalms 107 in the BOVCB

Psalms 107 in the BOYCB

Psalms 107 in the BPBB

Psalms 107 in the BPH

Psalms 107 in the BSB

Psalms 107 in the CCB

Psalms 107 in the CUV

Psalms 107 in the CUVS

Psalms 107 in the DBT

Psalms 107 in the DGDNT

Psalms 107 in the DHNT

Psalms 107 in the DNT

Psalms 107 in the ELBE

Psalms 107 in the EMTV

Psalms 107 in the ESV

Psalms 107 in the FBV

Psalms 107 in the FEB

Psalms 107 in the GGMNT

Psalms 107 in the GNT

Psalms 107 in the HARY

Psalms 107 in the HNT

Psalms 107 in the IRVA

Psalms 107 in the IRVB

Psalms 107 in the IRVG

Psalms 107 in the IRVH

Psalms 107 in the IRVK

Psalms 107 in the IRVM

Psalms 107 in the IRVM2

Psalms 107 in the IRVO

Psalms 107 in the IRVP

Psalms 107 in the IRVT

Psalms 107 in the IRVT2

Psalms 107 in the IRVU

Psalms 107 in the ISVN

Psalms 107 in the JSNT

Psalms 107 in the KAPI

Psalms 107 in the KBT1ETNIK

Psalms 107 in the KBV

Psalms 107 in the KJV

Psalms 107 in the KNFD

Psalms 107 in the LBA

Psalms 107 in the LBLA

Psalms 107 in the LNT

Psalms 107 in the LSV

Psalms 107 in the MAAL

Psalms 107 in the MBV

Psalms 107 in the MBV2

Psalms 107 in the MHNT

Psalms 107 in the MKNFD

Psalms 107 in the MNG

Psalms 107 in the MNT

Psalms 107 in the MNT2

Psalms 107 in the MRS1T

Psalms 107 in the NAA

Psalms 107 in the NASB

Psalms 107 in the NBLA

Psalms 107 in the NBS

Psalms 107 in the NBVTP

Psalms 107 in the NET2

Psalms 107 in the NIV11

Psalms 107 in the NNT

Psalms 107 in the NNT2

Psalms 107 in the NNT3

Psalms 107 in the PDDPT

Psalms 107 in the PFNT

Psalms 107 in the RMNT

Psalms 107 in the SBIAS

Psalms 107 in the SBIBS

Psalms 107 in the SBIBS2

Psalms 107 in the SBICS

Psalms 107 in the SBIDS

Psalms 107 in the SBIGS

Psalms 107 in the SBIHS

Psalms 107 in the SBIIS

Psalms 107 in the SBIIS2

Psalms 107 in the SBIIS3

Psalms 107 in the SBIKS

Psalms 107 in the SBIKS2

Psalms 107 in the SBIMS

Psalms 107 in the SBIOS

Psalms 107 in the SBIPS

Psalms 107 in the SBISS

Psalms 107 in the SBITS

Psalms 107 in the SBITS2

Psalms 107 in the SBITS3

Psalms 107 in the SBITS4

Psalms 107 in the SBIUS

Psalms 107 in the SBIVS

Psalms 107 in the SBT

Psalms 107 in the SBT1E

Psalms 107 in the SCHL

Psalms 107 in the SNT

Psalms 107 in the SUSU

Psalms 107 in the SUSU2

Psalms 107 in the SYNO

Psalms 107 in the TBIAOTANT

Psalms 107 in the TBT1E

Psalms 107 in the TBT1E2

Psalms 107 in the TFTIP

Psalms 107 in the TFTU

Psalms 107 in the TGNTATF3T

Psalms 107 in the THAI

Psalms 107 in the TNFD

Psalms 107 in the TNT

Psalms 107 in the TNTIK

Psalms 107 in the TNTIL

Psalms 107 in the TNTIN

Psalms 107 in the TNTIP

Psalms 107 in the TNTIZ

Psalms 107 in the TOMA

Psalms 107 in the TTENT

Psalms 107 in the UBG

Psalms 107 in the UGV

Psalms 107 in the UGV2

Psalms 107 in the UGV3

Psalms 107 in the VBL

Psalms 107 in the VDCC

Psalms 107 in the YALU

Psalms 107 in the YAPE

Psalms 107 in the YBVTP

Psalms 107 in the ZBP