Revelation 18 (BOGWICC)

1 Zitatha izi ndinaona mngelo wina akutsika kuchokera kumwamba. Iye anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero. 2 Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti:“ ‘Wagwa! Wagwa Babuloni Wamkulu!’Wasandulika mokhalamo ziwandandi kofikako mizimu yonse yoyipandi mbalame zonse zonyansandi zodetsedwa. 3 Pakuti mayiko onse amwavinyo ozunguza mutu wazigololo zake.Mafumu a dziko lapansi achita naye chigololo,ndipo amalonda a dziko lapansi analemera kuchokera pa zolakalaka zake zosefukira.” 4 Ndiponso ndinamva mawu ena kuchokera kumwamba akuti:“ ‘Anthu anga tulukani, mwa iye,’mungachimwe nayekuti musadzalandire nawo gawo lililonse la miliri yake; 5 pakuti machimo ake awunjikana mpaka kumwamba,ndipo Mulungu wakumbukira milandu yake. 6 Bwezerani Iye monga momwe iye anakuchitirani.Mubwezereni mowirikiza pa zimene anachita.Mumusakanizire magawo awiri kuchokera mʼchikho chake. 7 Mumuzunze, kumumvetsa chisoni kwambirimonga mwaulemerero ndi zolakalakazimene anadzaza mu mtima mwake. Iye anadzikuza nʼkumati,‘Ndinakhala monga mfumu yayikazi,ine sindine wamasiyendipo sindidzalira maliro.’ 8 Chifukwa chake miliri yake idzamugonjetsa tsiku limodzi;imfa, kulira maliro ndi njala.Iye adzanyeka ndi motopakuti wamphamvu ndi Mulungu Ambuye amene wamuweruza. 9 “Mafumu a dziko lapansi, amene anachita naye chigololo nachita naye pamodzi zosangalatsa moyo uno, akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzalira nakhuza maliro ake. 10 Iwo adzayima kutali nalira chifukwa choopsedwa ndi mazunzo ake.“ ‘Tsoka! Tsoka mzinda waukuluiwe, Babuloni mzinda wamphamvu!Mu ora limodzi chiwonongeko chako chafika!’ 11 “Amalonda a dziko lapansi adzalira nakhuza maliro ake chifukwa palibenso amene akugula katundu wawo, 12 katundu wagolide, siliva, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale; nsalu zoyera kwambiri zapamwamba ndi zofiira; nsalu zasilika ndi zapepo; mitengo iliyonse yonunkhira ndi zinthu zilizonse zopangidwa ndi mnyanga, kapena matabwa ogulidwa ndi ndalama zambiri kapena mkuwa kapena chitsulo ndi mwala wonyezimira; 13 zokometsera zakudya, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta a olivi, ufa wosalala ndi tirigu; ngʼombe ndi nkhosa; akavalo ndi ngolo; ndi anthu adzagulitsidwa ukapolo. 14 “Iwo adzanena kuti, ‘Chipatso chimene unachilakalaka chakuchokera. Chuma chako chonse ndi ulemerero zatha, sizidzapezekanso.’ 15 Amalonda amene anagulitsa zinthu izi napeza chuma kuchokera kwa iye adzayima patali potero ataopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kukhuza maliro 16 ndipo adzalira mokuwa kuti,“ ‘Tsoka! Tsoka! Mzinda waukulu,iwe wovala nsalu zoyera kwambiri, zapepo ndi zofiira,ndi wonyezimira ndi golide, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale! 17 Chuma chambiri choterechi chafika powonongeka mu ora limodzi!’“Oyendetsa sitima ndi onse oyenda pa sitima ya pamadzi, ogwira ntchito mʼsitima ndi onse amene amadalira nyanja pamoyo wa tsiku ndi tsiku adzayima patali potero. 18 Akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzakuwa kuti, ‘Kodi panalinso mzinda wina ngati mzinda waukuluwu?’ 19 Adzathira fumbi pamitu pawo ndipo adzalira nakhuza maliro kuti,“Tsoka! Tsoka mzinda waukulu iwe,kumene onse anali ndi sitima pa nyanjaanalemera kudzera mʼchuma chake!Mu ora limodzi wawonongedwa. 20 “Kondwerani chifukwa cha iye inu kumwamba!Kondwerani oyera mtimandi atumwi ndi aneneri!Mulungu wamuweruza iyemonga momwe anakuchitirani inu.” 21 Kenaka mngelo wamphamvu ananyamula mwala waukulu ngati mphero yayikulu nawuponya mʼnyanja nanena kuti,“Mwa mphamvu chonchimzinda waukulu wa Babuloni udzaponyedwa pansi,sudzapezekanso. 22 Mwa iwe simudzamvekanso liwu la woyimba zeze, ndi akatswiri a zoyimbayimba,oyimba zitoliro, ndi lipenga.Mwa iwe simudzapezekansomʼmisiri wina aliyense.Mwa iwe simudzapezekansophokoso la mphero. 23 Kuwala kwa nyalesikudzawunikanso mwa inu.Mawu a mkwati ndi mkwatibwisadzamvekanso mwa iwe.Amalonda anu anali akuluakulu a dziko lapansi.Mitundu yonse inasokonezedwa ndi zamatsenga zako. 24 Mwa iye munapezeka magazi a aneneri ndi a oyera mtima,ndi onse amene anaphedwa pa dziko lapansi.”

In Other Versions

Revelation 18 in the ANGEFD

Revelation 18 in the ANTPNG2D

Revelation 18 in the AS21

Revelation 18 in the BAGH

Revelation 18 in the BBPNG

Revelation 18 in the BBT1E

Revelation 18 in the BDS

Revelation 18 in the BEV

Revelation 18 in the BHAD

Revelation 18 in the BIB

Revelation 18 in the BLPT

Revelation 18 in the BNT

Revelation 18 in the BNTABOOT

Revelation 18 in the BNTLV

Revelation 18 in the BOATCB

Revelation 18 in the BOATCB2

Revelation 18 in the BOBCV

Revelation 18 in the BOCNT

Revelation 18 in the BOECS

Revelation 18 in the BOHCB

Revelation 18 in the BOHCV

Revelation 18 in the BOHLNT

Revelation 18 in the BOHNTLTAL

Revelation 18 in the BOICB

Revelation 18 in the BOILNTAP

Revelation 18 in the BOITCV

Revelation 18 in the BOKCV

Revelation 18 in the BOKCV2

Revelation 18 in the BOKHWOG

Revelation 18 in the BOKSSV

Revelation 18 in the BOLCB

Revelation 18 in the BOLCB2

Revelation 18 in the BOMCV

Revelation 18 in the BONAV

Revelation 18 in the BONCB

Revelation 18 in the BONLT

Revelation 18 in the BONUT2

Revelation 18 in the BOPLNT

Revelation 18 in the BOSCB

Revelation 18 in the BOSNC

Revelation 18 in the BOTLNT

Revelation 18 in the BOVCB

Revelation 18 in the BOYCB

Revelation 18 in the BPBB

Revelation 18 in the BPH

Revelation 18 in the BSB

Revelation 18 in the CCB

Revelation 18 in the CUV

Revelation 18 in the CUVS

Revelation 18 in the DBT

Revelation 18 in the DGDNT

Revelation 18 in the DHNT

Revelation 18 in the DNT

Revelation 18 in the ELBE

Revelation 18 in the EMTV

Revelation 18 in the ESV

Revelation 18 in the FBV

Revelation 18 in the FEB

Revelation 18 in the GGMNT

Revelation 18 in the GNT

Revelation 18 in the HARY

Revelation 18 in the HNT

Revelation 18 in the IRVA

Revelation 18 in the IRVB

Revelation 18 in the IRVG

Revelation 18 in the IRVH

Revelation 18 in the IRVK

Revelation 18 in the IRVM

Revelation 18 in the IRVM2

Revelation 18 in the IRVO

Revelation 18 in the IRVP

Revelation 18 in the IRVT

Revelation 18 in the IRVT2

Revelation 18 in the IRVU

Revelation 18 in the ISVN

Revelation 18 in the JSNT

Revelation 18 in the KAPI

Revelation 18 in the KBT1ETNIK

Revelation 18 in the KBV

Revelation 18 in the KJV

Revelation 18 in the KNFD

Revelation 18 in the LBA

Revelation 18 in the LBLA

Revelation 18 in the LNT

Revelation 18 in the LSV

Revelation 18 in the MAAL

Revelation 18 in the MBV

Revelation 18 in the MBV2

Revelation 18 in the MHNT

Revelation 18 in the MKNFD

Revelation 18 in the MNG

Revelation 18 in the MNT

Revelation 18 in the MNT2

Revelation 18 in the MRS1T

Revelation 18 in the NAA

Revelation 18 in the NASB

Revelation 18 in the NBLA

Revelation 18 in the NBS

Revelation 18 in the NBVTP

Revelation 18 in the NET2

Revelation 18 in the NIV11

Revelation 18 in the NNT

Revelation 18 in the NNT2

Revelation 18 in the NNT3

Revelation 18 in the PDDPT

Revelation 18 in the PFNT

Revelation 18 in the RMNT

Revelation 18 in the SBIAS

Revelation 18 in the SBIBS

Revelation 18 in the SBIBS2

Revelation 18 in the SBICS

Revelation 18 in the SBIDS

Revelation 18 in the SBIGS

Revelation 18 in the SBIHS

Revelation 18 in the SBIIS

Revelation 18 in the SBIIS2

Revelation 18 in the SBIIS3

Revelation 18 in the SBIKS

Revelation 18 in the SBIKS2

Revelation 18 in the SBIMS

Revelation 18 in the SBIOS

Revelation 18 in the SBIPS

Revelation 18 in the SBISS

Revelation 18 in the SBITS

Revelation 18 in the SBITS2

Revelation 18 in the SBITS3

Revelation 18 in the SBITS4

Revelation 18 in the SBIUS

Revelation 18 in the SBIVS

Revelation 18 in the SBT

Revelation 18 in the SBT1E

Revelation 18 in the SCHL

Revelation 18 in the SNT

Revelation 18 in the SUSU

Revelation 18 in the SUSU2

Revelation 18 in the SYNO

Revelation 18 in the TBIAOTANT

Revelation 18 in the TBT1E

Revelation 18 in the TBT1E2

Revelation 18 in the TFTIP

Revelation 18 in the TFTU

Revelation 18 in the TGNTATF3T

Revelation 18 in the THAI

Revelation 18 in the TNFD

Revelation 18 in the TNT

Revelation 18 in the TNTIK

Revelation 18 in the TNTIL

Revelation 18 in the TNTIN

Revelation 18 in the TNTIP

Revelation 18 in the TNTIZ

Revelation 18 in the TOMA

Revelation 18 in the TTENT

Revelation 18 in the UBG

Revelation 18 in the UGV

Revelation 18 in the UGV2

Revelation 18 in the UGV3

Revelation 18 in the VBL

Revelation 18 in the VDCC

Revelation 18 in the YALU

Revelation 18 in the YAPE

Revelation 18 in the YBVTP

Revelation 18 in the ZBP